KUCHEZEREDWA NDI MNGELO



Masomphenyawo amapitirira. Iye amauzidwa ndi azibusa amzake kuti masomphenya ake sanali ochokera kwa Mulungu. Iye anauzidwa kuti mzimu woyipa unamulowa iye. Izi zinamusautsa iye mwakuya. Kulemedwako kumakhala kochuluka kwambiri kuti angakupirire, chotero iye anapita ku tchire kuti akapeze Chifuniro cha Mulungu. Iye anali wodzipereka kwambiri mwakuti iye analumbira kuti sabwereranso wopanda yankho. Munali umo, mu kanyumba ka mphanga, mmene Mngelo wa Ambuye anamupatsa iye kutumidwa kwake. Pakati pa zinthu zina, Mngelo anamuuza iye izi: “Ngati iwe ukawapangitse anthu kuti akukhulupirire iwe, ndi kukhala woona mtima pamene iwe ukupemphera, palibe kanthu kati kadzaime pa mapemphero ako, osati ngakhale khansa.”

Kukaikira konse kunali kutachokapo. Iye tsopano anali nako kutumidwa ndipo molimba mtima anapita patsogolo. Chitsitsimutso cha machiritso chinali chitayambika.

Mazana zikwi zikwi amakhala nawo pa misonkhano yokopa anthu ya Branham. Zikwi zikwi zimachiritsidwa mu Dzina la Ambuye Yesu Khristu. Alaliki ena monga ngati Oral Roberts, T.L. Osborne, ndi A.A. Allen posakhalitsa anamutsatira M’bale Branham ndipo anayambitsa zitsitsimutso zawo za machiritso. Ambuye anavumbitsa pansi madalitso Ake moposa kale lonse. Dzanja lochiritsa la Yesu Khristu kamodzinso linali litakhudza anthu Ake.

“Ine nthawi zambiri ndimalira ndi chisangalalo chifukwa cha mphatso ya Mulungu ya posachedwapa kwa mpingo wa m’bale wathu wokondedwa, William Branham, ndi mphatso yake yodabwitsa ya machiritso. Izi ndi zochitika zakuti Mulungu akuchita zochuluka mowonjeza kuposa zonse zimene ife tingazipemphe kapena kuziganizira (Aefeso 3:20), chifukwa ine sindinayambe ndaziwonapo kapena kuwerengapo za chirichonse chofanana ndi utumiki wa machiritso wa William Branham.”

M’busa F.F. Bosworth, mlaliki wodziwika pa dziko lonse ndi mmodzi wa makolo oyambitsa chipembedzo cha Assemblies of God komanso modern Pentecostal movement.

“Mu chochitika chimodzi, ife tinawonerera pamene iye ankalankhula ndi bambo atagona pa machira. Poyambirira panalibe chisonyezo cha kuyankhira kwa nzeru kuchokera kwa bamboyo. Kenako kufotokoza kunabwera kuchokera kwa mkazake ataima pamenepo, kuti bamboyo sikuti anali akufa kokha ndi khansa, koma anali wogontha ndipo samatha kumva zimene zinali kunenedwazo.

M’bale Branham ndiye anati kunali kofunikira kuti bamboyo alandire kumva kwake ndi cholinga chakuti iye amufotokozere iye kuchiritsidwa kwa khansa yake. Pamenepo panali kamphindi ka pemphero. Mwadzidzidzi bamboyo amakhoza kumva! Misonzi yaikulu yonenepa inatsikira pansi mmasaya a bambo ameneyo amene nkhope yake usiku wonse inali yosatha kufotokoza ndi wosatha kulankhula. Iye amamvetsera ndi chidwi chakuya pamene iye ankauzidwa za kuwomboledwa kwake ku khansa.”

M’busa Gordon Lindsay, mlembi wodziwika, mtumiki, ndi woyambitsa wa Christ For The Nations Institute.

“M’bale Branham anati, ‘Congressman wachiritsidwa.’ Mtima wanga unalumpha. Ine ndinadzuka ndi kumuvomereza Ambuye ngati Mchiritsi wanga. Ine ndinaika pambali ndodo zanga…ndipo pansi pa Kumwamba panagwa!”

William D. Upshaw, US Congressman (1919-1927), woimira Uprezidenti wa US mu 1932. Analumala kuchokera pamene anagwa nathyola nsana wake ali mwana. Iye anali 84 pamene iye anachiritsidwa kwathunthu kuchokera ku pemphero la M’bale Branham, atakhala wolumala kwa zaka 66. Iye sanasowenso chikuku kapena ndodo zoyendera kwa moyo wake wonse.

“Ine ndinakhala chogona kwa zaka eyiti ndi miyezi naini ndiri ndi T.B. ndipo madokotala anali atandilephera. Ine sindimalemera ngakhale mapaundi 50 ndipo izo zinkawoneka kuti chiyembekezo chonse chinali chitapita. Ndiye kuchokera ku Jeffersonville, Indiana, kunabwera M’busa WM Branham mu masomphenya amene iye anali atawawona a mwanawankhosa akugwidwa ku nkhalango ndipo amafuula ‘Milltown,’ kumene kuli kumene ine ndimakhala. M’bale Branham anali asanayambe wabwerako kuno kapena kumudziwa aliyense wochokera kuno. Atabwera, iye anadzaika manja pa ine ndi kundipempherera, kumatchula pa ine Dzina la Ambuye wathu wokondedwa Yesu. Chinachake chimawoneka kuti chikundigwira ine ndipo nthawi yomweyo ndinadzuka ndikumuthokoza Mulungu chifukwa cha mphamvu Yake yochiritsa. Tsopano ndine woimba limba mu mpingo wa Baptisti kuno.”

Georgia Carter, Milltown Indiana, anachiritsidwa ku T.B. yosachiritsika mu 1940 ndipo sanadzadwalenso ku matenda amenewo tsiku lina mu moyo wake. Iyeyo akuimira zikwi makumi makumi za anthu amene achiritsidwa kudutsa mu utumiki wake ndipo akuchiritsidwabe mpaka lero.