LAWI LA MOTO



M’bale Branham kawirikawiri amalifotokoza Lawi la Moto limene linkatsimikizira Utumiki wake. Ilo linalipo pa kubadwa kwake, linawonedwa ndi zikwi zikwi pa gombe pa Mtsinje wa Ohio, ndipo linkawoneka kuti limamutsatira iyeyo kulikonse kumene iye ankapita. Munali mu 1950 pamene Ambuye anawapatsa onse okhulupirira ndi osakhulupirira mofanana chitsimikiziro chosalephera kuti Lawi la Moto ili linali ndi mneneri.

Usikuwo unaphimbidwa ndi kutsutsana ku Sam Houston Coliseum. M’bale Branham anali akutsogolera chitsitsimutso cha machiritso chimene chinali kusesa dzikolo. Madalitso a Ambuye Yesu anali kutsanuliridwa ngati mvula pa minda yauzimu ya tirigu. Koma zizindikiro zazikulu ndi zodabwitsa sizinangobwera popanda kutsutsidwa. Monga nthawiyonse, mdaniyo anadzutsa womenyana naye. Mphamvu ziwirizo zinakakomana ku Houston Texas, ndipo Mngelo wa Ambuye Mwiniwake anadzabwera yekha kuti adzamenye nkhondoyo.

Zikwi zikwi zinali zitafika kale kuti adzachitire umboni zozizwitsa zosawerengeka zimene zinkamutsatira munthu wa Mulungu uyu. Tsiku la pambuyo pake, gulu la azilaliki a komweko anamutsutsa mneneri kuti atsutsane pa machiritso Auzimu, koma chitsutsocho chinagwera kwa bwanawe wokhulupirika wokalamba wa mneneri, M’busa F.F. Bosworth. Otsutsa ambiri anatsogoleredwa ndi mtumiki wa komweko wa Baptist ndinso wotsutsa waphokoso wa machiritso Auzimu. Mtsutsano umene unali kubwerawo unaikidwa mmanyuzi pepala, amene mwamsanga anasindikiza nkhani zazikulu zikulu, “Ubweya wa Zaumulungu Uwuluka 7 Koloko usiku. Lero ku Sam Houston Coliseum.”

Wotsutsayo anamuchita ganyu katswiri wojambula, Ted Kipperman wa Douglas Studios, kuti adzajambule mtsutsanowo. Usiku umenewo, zithunzi zinajambulidwa ndi M’bale Bosworth ataima modzichepetsa pamene wotsutsayo amaima mokhala ngati monyogodola; nthawi ina anali atasonya chala chake pa nkhope ya bambo wachikulire wodzichepetsayo.

Pamene mtsutsanowo unayambika, M’busa Bosworth mwamsanga anatsimikizira kutsimikizika kwa machiritso Auzimu ndi umboni wa Mwamalemba ndiyeno, kuti asasiye funso lirilonse, anawafunsa onse amene anachiritsidwa ku zifooko zawo kuti aimirire. Zikwi zikwi anaimirira kumapazi awo. Pamene iwo amene anachiritsidwawo anakhala pansi, iye anafunsanso iwo onse amene anachiritsidwa ndi machiritso Auzimuwo amene anali mamembala okhazikika mu chipembedzo cha bambo uyu kuti aimirire. Mamembala a tchalitchi firii handiredi anaimirira kuti awonetsere monyadila chifundo chimene Ambuye Yesu anali atawasonyezera iwo.

Kutsutsa ndiye kunabwera kuchokera kwa wotsutsayo. “Muloleni mchiritsi Wauzimu uja abwere pano. Muloleni iye adzawonetsere.” M’bale Bosworth anali atanena mwachimvekere kuti Yesu anali Mchiritsi Wauzimu yekhayo, koma kulalata kuchokera kwa wotsutsayo kunapitirira. Potsiriza, M’bale Bosworth anamuitanira M’bale Branham kuti abwere pa nsanja. Iye anavomereza kuitanako ndipo anabwera pa nsanja mkati mkati mwa kufuula kwa ogwirizana nazo.

Mneneri, atadzozedwa ndi Mzimu Woyera, anapereka kuyankhira kotsatiraku:

Ine sindingathe kumuchiritsa aliyense. Izi ine ndimazinena. Pamene ine ndinali ka khanda kobadwira ku Mzinda wa Kentucky, mogwirizana ndi zonena za amayi anga okondedwa, ndi zimene zatsimikiziridwa kudutsa mmoyo wanga, panali Kuwala kumene kunabwera mchipinda cha kanyumba kakang’ono kakale ako, kumene iko kanali, munali mosazila mmenemo, kanalibe ngakhale zenera, iwo anangokhala ndi kanthu kakang’ono kakale ngati zenera pamenepo, kokhala ngati chitseko chaching’ono, ndipo iwo anachikankha icho kuti chitseguke pafupifupi faifi koloko mmawa, ndipo Kuwala uku kunadzazungulira kukalowa pamene tsiku linali kucha. Chiyambireni nthawi imeneyo, Iko kwakhala kuli ndi ine. Iko ndi Mngelo wa Ambuye. Iye anakomana nane ine maso ndi maso zaka pang’ono zapitazo. Kudutsa mmoyo wanga, Iye wakhala akundiuza ine zinthu zimene zimadzachitika, ndipo ine ndimazinena izo chimodzimodzi basi monga Iye amandiuzira ine. Ndipo ine ndikutsutsa aliyense pa malo aliwonse, kuti apite ku mzinda kumene ine ndinakulira, kapena kwina kulikonseko, ngati ndinanenapo mawu mu Dzina la Ambuye, koma zimene zimachitika ndendende mmene izo zinanenedwera kuti zikanadzachitikira.

Iye atatha kunena mawu amenewo, Mzimu Woyera unadzagwa pa nsanjapo, ndipo wojambula wotengekayo anajambula chithunzi. M’bale Branham anachoka pa nsanjapo ndi maneno ophweka, komabe auneneri: “Mulungu achitira umboni. Ine sindinenanso zina.”

Mzawo wa Bambo Kipperman mwamsanga anapita kumakatsuka zithunzizo kuti zikatuluke mu nyuzi ya mmawa wotsatira. Iye anazindikira chinachake chododometsa pamene iye amachotsa chithunzi choyamba kuchokera mu mankhwala otsukirawo. Izo, monga zithunzi zisanu zotsatira, zinali zopanda kanthu. Iye anagwira mtima wake ndipo anagwera chamtsogolo pamene iye amasolola chithunzi chake chomaliza kuchokera mmankhwalawo. Apo, pa chithunzi chotsirizira icho, panali Lawi la Moto mmawonekedwe owonekera chitaima pa mutu wa mneneri wa Mulungu, William Marrion Branham.

Ana a Israeli anachitira umboni Lawi la Moto likumutsogolera Mose, ndipo anthu a tsiku lamakono lino achitiranso umboni Lawi la Moto lomwe lija likumutsogolera mneneri wina.