LONJEZO LA MNENERI M’MASIKU OMALIZA



Mawu omalizira kumene amene analembedwa mu Chipangano Chakale akupereka lonjezo ili: “Taonani, ine ndidzakutumizirani inu Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi lowopsya la AMBUYE: Ndipo iye adzatembenuza mtima wa atate kwa ana, ndi mtima wa ana kwa atate awo, kuti ndingadze ndi kulikantha dziko lapansi ndi themberero.” (Malaki 4:5-6)

Tsiku lalikulu ndi lowopsya la Ambuye ndi lakuti libwerabe mtsogolo, kotero modzipereka ife tidziyembekezera mneneri Eliya. Mu Baibulo, aneneri sankabwera ku mabungwe azipembedzo zazikulu. Iwo ankabwera kwa osankhidwa apang’ono. Talingalirani ngati zitakhala kuti mneneri wa Malaki 4 anabwera, ndipo iye anaphonyedwa. Nanga bwanji ngati iyeyo ali monga aneneri akale, ndipo anthu apang’ono okha anamuzindikira iye? Ngati mneneri uyu ali woti adzabwerera mu tsiku lomaliza, kodi ife tidzamudziwa bwanji iye? Yankho lake likuwonekera poyera mu Malemba. Iyeyo adzakhala ndi chikhalidwe cha mneneri. Iye azidzadziwa zinsinsi za mu mtima. Iye azidzachita zozizwitsa. Mabungwe achipembedzo adzayesera kuti amuchepsye iye. Koma apo padzakhala osankhidwa apang’ono amene ati adzamuzindikire iye ngati mtumiki wolonjezedwa wa tsikuli.

Kodi ife tidzadziwa bwanji Eliya akamadzabwerera? Kodi iye adzawonetsera makhalidwe otani, kuti ife tidzakhoze kumuzindikira iye?

Eliya anali mwamuna wa ku chipululu. Zizindikiro zazikulu ndi zodabwitsa zinatsatira utumiki wake. Iye analalikira motsutsa zoyipa za tsiku lake. Iye makamaka analalikira motsutsa makhalidwe oyipa a Mfumukazi Yezebeli. Pamene Eliya ankatengedwa kupita Kumwamba mu galeta la moto, mzimu wake unagwera pa Elisha. Zizindikiro zazikulu ndi zodabwitsa kenako zinatsalira pa utumiki wa Elisha, ndipo nayenso analalikira motsutsa machimo a dziko lapansi. Aneneri onsewo anaima okha motsutsa mabungwe achipembedzo a tsiku limenelo. Zaka mazana kenako, mzimu womwewo unadzabwerera pa dziko lapansi mwa Yohane M’batizi. Mneneri Malaki ananeneratu kuti Eliya akanadzabwerera kuti adzamusonyeze Ambuye: Taonani, ine ndidzatuma mtumiki wanga, ndipo iye adzakonzekeretsa njira pamaso panga… (Malaki 3:1). Yohane M’batizi anali atakwanira pamene iye ankanena za kulapa pakati pa ana a Mulungu. Monga Eliya, iye analalikira motsutsa mfumu ndi zipembedzo za mabungwe zamakono. Ambuye Yesu anatsimikizira kuti Yohane M’batizi anali mneneri wa Malaki 3 mu Bukhu la Mateyu (11:10): “Pakuti uyu ndi iyeyo, amene zinalembedwa za iye, Taonani, ine ndidzatumiza mtumiki patsogolo pako, amene ati adzakonzekeretse njira pamaso pako.” Luka 1:17 amanena kuti mzimu wa Eliya (Elias) unkayenera kudzakhala mwa Yohane M’batizi, Ndipo iye adzapita patsogolo panu mu mzimu ndi mu mphamvu za Eliya, kuti akabwezeretse mitima ya atate kwa ana. Koma zindikirani kuti gawo lachiwiri la Malaki 4 linali loti lidzakwaniritsidwabe: …ndi mtima wa ana kwa atate awo, kuti ine ndingadze ndi kudzawononga dziko lapansi ndi themberero. Gawo ilo la Lemba lidzayenera kuti lidzakwaniritsidwe kusanafike Kudza Kwachiwiri kwa Khristu.

Zaka thuu sauzande Yohane M’batizi atachoka, yafikanso nthawi panonso kuti mzimu wa Eliya ubwerere pa dziko lapansi.

Tsiku limenelo lafika! Mu m’badwo uno, ife tawuwona mzimu wa Eliya ukubwerera. Iye anatsutsa kachitidwe ka chipembedzo kamakono. Iye anaima motsutsa machimo a dziko lapansi. Iye anasonyeza zizindikiro ndi zodabwitsa zosawerengeka. Iye analalikira Baibulo mawu-pa-mawu kuyambira ku Genesis mpaka ku Chivumbulutso. Mneneri wa Malaki 4 anabwera monga kunalonjezedwa, ndipo iye anabweretsa Uthenga kuchokera pa Mpandowachifumu wa Mulungu Wamphamvuzonse. Dzina la mneneri ameneyo ndi William Marrion Branham. Ife timamutcha iye “M’bale Branham.”

“William Branham, amene ine ndimamukonda ndi kumukhulupirira kuti anali mneneri wa Mulungu.”

Oral Roberts, Mlaliki wodziwika pa dziko lonse ndi Mwiniwake wa Oral Roberts University.

“William Branham anabwera kwathu kuno ngati mneneri wa Mulungu ndipo anadzatisonyeza ife mu zaka zana za mmatwente ndendende zinthu zomwe zomwezo zimene ife tinasonyezedwa mu Mauthenga…Mulungu wawachezera anthu Ake, pakuti mneneri wamphamvu wawuka pakati pathu.”

Dr. T.L. Osborne, mlaliki wa Chipentekoste ndi mlembi wodziwika.

“Asanayambe kumupempherera munthu, iye ankakhoza kupereka mfundo zolondola zokhudza kudwala kwa munthuyo, ndiponso zochitika za miyoyo yawo - kumene iwo akuchokera, zochitika, zochita zawo - ngakhale mmbuyo kumene ku ubwana wawo. Branham sanayambe waphonyetsapo ndi mawu achidziwitso mu zaka zonse zimene ine ndinakhala ndi iye. Zimenezo, kwa ine, zinali zochitika zikwi zikwi.”

Ern Baxter, mlaliki, manenjala wa Misonkhano yokopa anthu ya Branham kwa zaka seveni, ndiponso mmodzi wa atsogoleri oyamba a British New Church Movement.

Chiyendereni Ambuye Yesu Khristu pa dziko lapansi sipanayambe pakhalapo munthu amene analikhudza dziko lapansi mwanjira yodabwitsa chotero. Kuchokera ku mayambidwe ophweka mu kanyumba ka chipinda-chimodzi ku mapiri a Kentucky, mpaka ku Amarillo Texas kumene Ambuye anamutengera iye kuti azipita kwawo, moyo wake unali mosalekeza wodzaza ndi zochitika zauzimu. Molangizidwa ndi Mngelo wa Ambuye mu 1946, utumiki wa M’bale Branham unakhethemula moto umene unayatsa nthawi ya zitsitsimutso zazikulu za machiritso zimene zinasesa kudutsa Amereka ndi kuzungulira dziko lapansi. Mpaka tsiku la lero, iye akudziwidwa ndi azambiriyakale a Chikhristu ngati “tate” ndi “wotsogolera” wa chitsitsimutso cha machiritso cha m’ma 1950 chimene chinausintha Mpingo wa Chipentekoste ndiponso mokhazikika kuwukitsa kuyenda kwa Zachipembedzo, zimene lero zikukopa pafupifupi chipembedzo chirichonse cha Chiprotestanti. Komabe, zoona zake nzakuti, azipembedzo samaziwerengera zophunzitsa zake ndipo amakana kutumidwa kwake.

Kulikonse kumene iye amapita, Mulungu ankatsimikizira kuti M’bale Branham ndi mneneri wa m’badwo uno. Monga Yobu, Ambuye analankhula ndi iye mu kamvulumvulu. Monga Mose, Lawi la Moto linkawoneka likumutsogolera iye. Monga Mikaya, iye ankadedwa ndi azibusa. Monga Eliya, iye anali munthu wa kuthengo. Monga Yeremiya, iye anatumidwa ndi Mngelo. Monga Daniele, iye ankawona masomphenya a za mtsogolo. Monga Ambuye Yesu, iye ankadziwa zinsinsi za mu mtima. Ndipo monga Paulo, iye ankachiritsa odwala.

Ambuye panonso wawachezera anthu Ake kudzera mwa mneneri. Mu nthawi ya mdima mu mbiriyakale, pamene makhalidwe atsika mwakuya mwakuti sizinayambe zawonekapo ndipo zida zakupha khwimbi la anthu zaikidwa mu mlengalenga, munthu wodzichepetsa anatumizidwa kuchokera pamaso pa Mulungu kuti akawuitanire mtundu wa anthu wakufa ku kulapa.

Wophunzira wokondedwa Yohane analemba za Ambuye Yesu: Ndipo ziriponso zinthu zina zambiri zimene Yesu anachita, zimene, ngati izo zikanati zilembedwe zirizonsezo, ine ndikuganiza kuti ngakhale dziko lomwe silikanakhoza kusungira mabuku amene akanalembedwa. Ameni. (Yohane 21:25)

Zomwezonso zikhoza kunenedwa za moyo wa M’bale Branham. Alipo maulaliki oposa 1,200 ojambulidwa pa tepi ndi zikwi zikwi za nkhani zokhudza moyo wa mwamuna wamphamvu uyu. Komabe ife tikumamvabe mosalekeza maumboni atsopano a chikoka chake pa miyoyo mamilioni a anthu. Ka bukhu aka sikangakhoze nkomwe kukanda pamwamba pa kukhudza kumene mwamuna uyu wa Mulungu anali nako pa dziko lapansi.