Awa ndi ena mwa mafunso omwe takhala tikulandira okhudzana ndi utumiki wathu. Ngati, mutatha kuwerenga izi, mukhalabe ndi funso pa zomwe zili pa webusaiti iyi, chonde titumizireni ife imelo pa answers@themessage.com.

 

Chikhulupiriro chanu chimanena chiyani?

Ife tikhoza kunena kuti chiphunzitso chathu “chodziwika” cha mpingo ndi Baibulo, kuchokera ku Genesis mpaka ku Chivumbulutso. Chonena chathu cha chikhulupiriro chathu chikhoza kulongosoledwa monga chonchi: Tiribe kachikhulupiriro koma Khristu; tiribe lamulo koma chikondi; tiribe bukhu koma Baibulo.

Ndine Mkhristu kale. Kodi zimene ziri pa webusaiti iyi ndi zaphindi kwenikweni kwa ine?

Inde! Akhristu ayenera kukhulupirira mawu onse a Mulungu; ndi chifukwa chake ife timapita ku tchalitchi ndi kumawerenga ma Baibulo athu. Ndi chifukwa chiyani inu mumakhulupirira gawo la Baibulo limene limanena kuti Yesu anafera machimo athu, ndipo nkusasamala za momwe tchimo linayambira M’munda wa Edeni?

Ine ndikukhulupirira kuti zimene ndawerengazi ndi zoona. Kodi ine ndingajowine bwanji?

Thupi la Khristu si mwambo kapena chipembedzo, ndipo chofunikira chokhakho kuti mukhale membala ndikuti mukhulupirire pa Ambuye Yesu Khristu. Musadandaule ndi zokhala wozindikiridwa kapena kulembetsa mmapepala a kayendetsedwe ka tchalitchi. Mungokhulupirira Mawu, ndipo Ambuye adzasamala zina zonsenso.

Kodi ndinu mpingo?

Ife sitiri bungwe la mpingo, koma ife timatumikira mipingo zikwi zikwi ndi anthu mamilioni kuzungulira pa dziko lapansi powapatsa iwo zowerenga zauzimu. Ntchito yathu ndi yakuti tiziwalimbikitsa anthu kuti akasendere pafupi ndi Ambuye Yesu pakuwupangitsa Uthenga Wake kuti uzipezeka kwa wina aliyense pa dziko lapansi.

Ine ndikufuna kuti ndibatizidwe. Tsopano nditani?

Ngati inu mukulephera kuti mumupeze winawake woti akubatizeni inu mu Dzina la Ambuye Yesu Khristu, titumizileni ife imelo ndi kunena kumene mukukhala ndipo tidzakutumizirani mndandanda wa matchalitchi omwe ali kwanuko amene angakubatizeni inu molondola. Kumbukirani, molingana ndi Baibulo ndi kofunikira kuti mubatizidwe mu Dzina la Yesu, ndipo osati mmaudindo a Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera.

Kodi inu mukuganiza kuti ine ndatayika chifukwa ndine wa Katolika kapena membala wa chipembedzo china?

Ambuye Yesu anati, “Musaweruze, kuti inunso musadzaweruzidwe.” Palibe munthu amene ali ndi ulamuliro woweruza chipulumutso. Yesu nayenso anati, “Iye amene akhulupirira ndipo nabatizidwa adzapulumutsidwa; koma iye amene sakhulupirira adzawonongedwa.” Kotero ziribe kanthu kaya ndiwe wa Katolika, Baptisti, kapena Pentekoste; ngati ukukhulupirira pa Ambuye Yesu Khristu ukatero udzapulumutsidwa.

Kodi Voice of God Recordings (VGR) ndi chiyani?

Voice Of God Recordings, Inc. ndi utumiki wa zipembedzo zonse umene wadzipereka kuti upititse patsogolo Uthenga wa Ambuye Yesu Khristu. Gwero lenileni la zipangizo zimene ife timagawa ndi maulaliki ojambulidwa a malemu William Marrion Branham, mneneri wa Mulungu ndi mlaliki wodziwika pa dziko lonse. Zimene timafikira nazo kwa anthu ndi ma CD a MP3, ma DVD, mavidiyo, maulaliki okhoza kuwerengedwa pa kompyuta, mabukhu, magazini, matraki, zithunzi, nyuzipepala, ndi webusaiti.

Kodi William Branham ndi ndani, ndipo kodi iyeyo ali ndi chochita chanji ndi ine?

M’busa Branham anali mlaliki wodziwika pa dziko lonse lapansi amene anali pa ntchito ya umishonare kuyambira mu 1947 mpaka 1965. Sikuti anangotsogolela kokha mamilioni kwa Khristu, koma Mulungu anawutsimikizira utumiki wake ndi zozizwitsa zosawerengeka. Mukapita apa pakupatsani inu malonje a ku utumiki wake

Ngati zozizwitsa zonsezi zimachitikadi, zikutheka bwanji kuti ine sindinayambe ndamvapo za iye?

Limenelo ndi funso labwino, ndiponso ndi limene ife tingafune kuti tiwafunse matchalitchi akulu akulu onsewa lero. Mulungu anatumiza mneneri! Ndi chifukwa chiyani aliyense sakukamba za zimenezo? Iwo akuyenera kutero.

Ndi chifukwa chiyani inu mumakokomeza kwambiri pa William Branham?

Pa chifukwa chomwecho chimene Yoswa ankakokomeza kwambiri za Mose. Mose anali mneneri amene anabweretsa Uthenga kuchokera kwa Mulungu. M’bale Branham ankachita chinthu chomwe chomwecho.

Ine ndawawona akazi amene ali mu utumiki wanu. Ndi chifukwa chiyani iwo onse ali ndi tsitsi lalitali ndipo amavala masiketi aatali?

Paulo ananena mu l Akorinto 11:15: Koma ngati mkazi aweta tsitsi, ndi ulemerero kwa iye: pakuti tsitsi lake lapatsidwa kwa iye ngati chophimba. Paulo ananenanso kuti akazi aziveke okha ndi zovala za ulemu… ndipo Mose anati, Mkazi asavale chovala cha mwamuna. Ngati Baibulo limanena zimenezi, ndiye kuti Akhristu owona azizikhulupirira zimenezo.

Ine ndinachita kafukufuku ndipo ndinapeza ma webusaiti angapo amene ntchito yake ndi kutsutsa zinthu zimene M’busa Branham amanena. Inu mumawayankha bwanji iwo?

Inu muziwapeza ma webusaiti amene ntchito yake ndi kutsutsa chirichonse ndi zonse, kuphatikizapo Baibulo. Ife mophweka tikungokupemphani inu kuti muweruze Uthenga umene tawupereka kwa inu mwa Mawu a Mulungu, ndipo osati mwa mbalume zimene zimakhala zophweka kwambiri kuzipeza pa intaneti. Kumbukirani, palibe wina amene ananyozedwa kwambiri ngati Ambuye Yesu Khristu. Ngati iwe ukuchita chinachake molondola, ndiye iwe ukhoza kumayembekezera kutsutsidwa.

Mabungwe onse ayika manja awo mmatumba mwanga. Nthawizonse zikumakhala za ndalama.

Mukhoza kuwona kuti palibepo malo pa webusaiti iyi poti muperekerepo chithandizo. Pamene idzafike nthawi yoti tikuyamba kupempha ndalama, ndiye kuti nthawi idzakhala itafika yoti utumiki uwu uthe. Izi si za ndalama, izi ndi zotengera miyoyo kwa Yesu Khristu.

Ine ndikufuna kuti ndiphunzire zambiri; kodi ndichite chiyani?

Baibulo limanena kuti, “chikhulupiriro chimadza pakumva,” kotero ife tikukulimbikitsani inu kuti mupitirize kumamvetsera. Ife tiri nawo maulaliki ojambulidwa oposa 1,200 omwe mungawapeze mwaulele. Ife tikhoza kukutumizirani inu mabuku ku positi ofesi ngati inu mukuvutika kuti muzipeze pozitenga pa intaneti.


www.branham.org imaika nkhani za tsiku ndi tsiku ndi maumboni ogwirizana ndi utumiki wathu. Ife tikukuitanani inu kuti mudzifikako tsiku lirilonse ndi kuwerenga malipoti ochokera kwa okhulupirira pa dziko lonse. Inu mukhoza kudabwitsidwa ndi kuchuluka kwa zinthu zopambana zimene Ambuye Yesu akuchita pakali pano, mu tsiku la makono lino.