MNENERI?Mu Baibulo, Mulungu nthawizonse ankabweretsa Uthenga Wake kwa anthu a pa dziko lapansi podzera mwa mneneri wa m’badwowo. Iye analankhula ndi Mose kudzera mu chisamba choyaka moto ndipo anamupatsa iye utumiki wakuti akawatsogolere Ahebri kuwatulutsa mu Igupto. Lawi la Moto lochita kumawoneka ndi zizindikiro zina zinaperekedwa kuti zikatsimikizire utumiki wake. Yohane M’batizi anabweretsa Uthenga wolikonzekeretsa dziko lapansi kwa Mesiya wakudzayo. Pamene anali kumubatiza Ambuye Yesu mu Mtsinje wa Yorodani, Liwu lochokera Kumwamba linatsimikizira utumiki wa Yohane kuti unali womusonyeza Mwanawankhosa wa Mulungu, “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, mwa yemwe Ine ndikondwera naye.” Zaka mtsogolo mwake, Liwu la Ambuye linadzamvekanso likulankhula kwa mneneri pamene Iye ankalankhula kwa Paulo kudzera mu Kuwala kochititsa khungu, ndipo kenako anamupatsa iye utumiki kuti akaikhazikitse mipingo mu dongosolo. Kudutsa mu Chipangano Chatsopano ndi Chakale, Mulungu sanayambe walankhulapo ndi anthu Ake kudzera mu kachitidwe kachipembedzo kapena bungwe la chipembedzo. Iye nthawizonse wakhala akulankhula kwa anthu podzera mwa munthu mmodzi: Mneneri Wake. Ndipo Iye amawatsimikizira aneneri amenewa podzera mu zizindikiro zauzimu.

Koma nanga bwanji lero? Kodi Mulungu akuululabe Mawu Ake kwa aneneri? Kodi zikadalipobe zizindikiro zauzimu? Kodi Mulungu angatumize mneneri wa tsiku-lamakono ku dziko lapansi? Yankho lake ndi lodziwikiratu kwambiri, “Inde!”

Koma kodi ife tidzadziwa bwanji pamene mneneriyo waturukira? Kodi iyeyo azidzawoneka motani? Kodi iyeyo azidzachita motani? Kodi iyeyo adzatipatsa ife chizindikiro chotani? Kodi iyeyo adzakwaniritsa Malemba ati?

Aneneri akale anali amuna amphamvu a Mulungu, ndipo sankawopa kuima motsutsana ndi mabungwe azipembedzo. Kunena moona, iwo nthawizonse ankakhala onenedwa ndi azibusa. Eliya anazitsutsa zipembedzo zamabungwe za tsiku lake, anawafunsa iwo ngati Mulungu angalemekeze nsembe yawo, kapena yake. Iwo anafuula. Iwo analosera. Iwo analumphira pamwamba pa guwa. Iwo anazidula okha ndi mipeni. Koma Mulungu sanawamve iwo. Eliya anayang’ana mmwamba Kumwamba ndipo anati, “Mulole chidziwike lero kuti inu ndinu Mulungu mu Israeli, ndipo kuti ndine wantchito wanu, ndipo kuti ine ndachita zinthu zonse izi pa mawu anu.” Atatelo iye anaitanitsa moto kuti utsike kuchokera Kumwamba ndi kudzanyeketsa nsembeyo. Mikaya mneneri anatsutsana ndi Mfumu ya Israeli, ndi unsembe wonsewo, pamene iye anamudzudzula Wansembe Wamkulu Zedekiah chifukwa chonenera bodza. Wansembe Wamkuluyo anamubwanyula iye kumaso ndipo Mfumu inakamuika iye mu ndende chifukwa chonena zoona. Ngakhale Ambuye Yesu ankadedwa kwambiri ndi mabungwe achipembedzo a tsiku Lake mpaka mwakuti iwo anamupachika Iye limodzi ndi zigawenga zowopsya kwambiri. Ngati mbiriyakale ili yowona, mneneri adzakhala wodedwa ndi kachitidwe kamakono ka chipembedzo, ndipo iye akhoza kutengedwa ngati wa mpatuko, mneneri wabodza, kapena zoposera pamenepo. Koma Mulungu adzaima ndi wantchito Wake.

Ngati pangakhale mneneri mu tsiku la makono lino, kodi iyeyo angavomerezedwe chotani ndi Mpingo wa Katolika? Mpingo wa Baptisti? Mpingo wa Chilutera? Chipembedzo chirichonsecho?

Ambuye Yesu anawatuma onse omukhulupirira Iye: “Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo amene akhulupirira; Mu dzina langa iwo azidzaturutsa ziwanda; iwo azidzalankhula ndi malirime atsopano; Iwo adzatola njoka; ndipo ngati iwo adzamwa chinthu chakupha chirichonse, icho sichidzawapweteka iwo; iwo adzaika manja pa odwala, ndipo iwo adzachira.” (Marko 16:17-18). Kodi Lemba ili ndi loona lero? Ngati ilo siliri loona, ndi liti pamene Mawu a Ambuye anaguga? Mu Baibulo lonse, aneneri amatha kuchiritsa odwala, kuturutsa ziwanda, ndi kuchita zozizwitsa. Mose anaikweza njoka ya mkuwa pamaso pa Israeli kuti iziwachiritsa iwo akalumidwa ndi njoka zaululu (Numeri 21:9). Namani, Msiriya wamphamvu, anabwera kwa Elisha kuti adzachiritsidwe ku khate (II Mafumu 5:9). Pamene mnyamata anagwa ndi kufa kuchokera pa zenera lapamwamba, mtumwi Paulo anamukumbatira iye ndipo anawubwezeretsanso moyo mu thupi lakufalo (Machitidwe 20:10). Ife tangokhala ndi zolembedwa za pafupifupi zaka zitatu ndi theka za moyo wa Ambuye Yesu, koma mu zaka pang’ono zimenezo, Iye mopitirira anakhala akuchiritsa odwala. Akhungu amapenyetsedwa. Akhate amachiritsidwa. Ogontha amalandira kumva kwawo. Olumala amayenda. Mtundu uliwonse wa matenda umachiritsidwa (Mateyu 4:23).

Mulungu ankawatsimikiziranso aneneri ake mu njira zosiyanasiyana pambali pa machiritso. Ngakhale zinsinsi zotchingidwa kwambiri za mu mtima zinkawululidwa kwa amuna awa a Mulungu. Mfumu Nebukadinezara anali ndi loto lomuvutitsa, koma iye samatha kukumbukira kuti izo zinali chiyani. Mneneri Danieli anamuuza mfumu ziwiri zonse lotolo ndi uneneri umene unadzatsatira (Daniele 2:28). Palibe chimene chinabisidwa kwa Solomoni pamene Mfumukazi yaku Sheba inabwera pamaso pa iye. Iye anali atadzazidwa kwambiri ndi Mzimu mwakuti iye anamuuza iye mafunso a mtima wake iye asanawafunse nkomwe iwo (I Mafumu 10:3). Elisha anamuuza Mfumu yaku Israeli zonse zomwe inkakonza Mfumu yaku Syria, ngakhale mawu a mseri amene ankalankhulidwa ku chipinda chake (II Mafumu 6:12).

Kupyolera mu zochita Zake zomwe, Ambuye Yesu kawirikawiri amasonyeza kuti Mzimu uwu wozindikira za mu mtima ndi Mzimu wa Khristu. Iye anazindikira chibadwa cha Nataniele pamene Iye anati, “Taonani mu Israeli weniweni, amene mwa iyeyo mulibemo chinyengo!” Ndipo Yesu anapitirira kumuuza Nataniele kumene iye anali pamene Filipo ankamuuza iye za Mesiya (Yohane 1:48). Pamene Nataniele anawona kuti Yesu anawudziwa mtima wake, iye nthawi yomweyo anamuzindikira Iye kuti ndi Khristu. Nthawi yoyamba imene Yesu anamuwona Petro, Iye anamuuza iye dzina la abambo ake, a Yonasi (Yohane 1:42). Petro pomwepo anasiya zonse ndipo anamutsatira Yesu moyo wake wonse. Yesu anakomana ndi mkazi wachi Samariya pa chitsime ndipo anamuuza iye za machimo ake akale. Mawu ake oyambirira anali, “Bwana, ine ndazindikira kuti inu ndinu mneneri” (Yohane 4:19). Anthu atatu onse awa anali ochokera ku mayendedwe osiyana a moyo, komabe mwamsanga iwo anamuzindikira Yesu pamene Iye anasonyeza mphatso ya kuzindikira za mumtima.

Kodi mphatso iyi inasowa pamene tsamba lomaliza la Baibulo linalembedwa? Ngati zozizwitsa izi zinalembedwa mosabisa mu Baibulo, kodi izozo ziri kuti lero? Mneneri wa tsiku la makono ndithudi adzatsimikiziridwa ndi zozizwitsa.

Kodi Mulungu wawaiwala anthu Ake? Kodi Iye akukhozabe kuchiritsa odwala? Kodi Iye akulankhulabe kwa ife kudzera mwa aneneri Ake? Kodi aliyense wa aneneri analiwoneratu tsiku la lero?

Kodi akadalipobe mauneneri amene ali woti akwaniritsidwebe lero?