ZINSINSI KUWULULIDWA



Koyambirira kwa utumiki wa M’bale Branham zinafika powonekeratu kuti kachitidwe ka chipembedzo kanamangidwa kuti kazithandizira mabungwe achipembedzo, ndipo osati Uthenga woona. M’bale Branham ankakhulupirira Baibulo Mawu pa Mawu, ndipo samanyengerera, ngakhale zitanthauza kuti azisalidwa ndi azimzake, abwenzi, kapena banja.

Pamene anali akadali membala wa Mpingo wa Missionary Baptist, iye anawuzidwa kuti awadzoze atumiki achikazi. Komabe, iye ankawadziwa bwino malemba onse. I Timoteo 2:12 mwachimvekere amati, “Koma ine sindilola kuti mkazi aphunzitse, kapena kukhala ndi ulamuliro pa mwamuna, koma kuti akhale chete,” ndipo I Akorinto 14:34 amati, “Mulole akazi anu akhale chete mu mipingo: pakuti sikuloledwa kuti iwo alankhule…” Uku sikunali kulimbana ndi akazi, koma Baibulo linali lomveka bwino pa phunzirolo. Pamene chigamulo chinaperekedwa, iye sakanatha kunyengerera chotero iye anachoka pa mpingopo.

Limenelo silinali Lemba lokhalo limene silimasamalidwa kwathunthu ndi zipembedzo. Ambuye anawulula choonadi pa ubatizo kwa M’bale Branham. Zinatheka bwanji kuti Yesu anawalamulira, “Pitani inu chotero, ndipo mukawaphunzitse mafuko onse, kuwabatiza iwo mu dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera,” komabe ubatizo uliwonse umene unalembedwa mu Baibulo umakhala mu Dzina la Yesu? Mtumwi Petro anawalamulira mu Machitidwe 2:38 kuti alape ndipo abatizidwe mu Dzina la Yesu Khristu. Malemba amagwira ntchito mu chiyanjano changwiro, koma izo zinatengera mneneri kuti awulule chinsinsi ichi: “Atate” si dzina, “Mwana” si dzina, ndipo “Mzimu Woyera” si dzina. Chimodzimodzi monga mmene mwamuna aliri atate wa ana ake, mwana kwa makolo ake, ndi mchimwene kwa azibale ake, komabe dzina lake si “atate,” “mwana,” kapena “mchimwene.” Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera ndi maudindo a Dzina la Yesu Khristu. Mateyu 28:19 ndi Machitidwe 2:38 anabwera mogwirizana mwangwiro.

Ngakhale tchimo la pachiyambi m’Munda wa Edeni linawululidwa, osati monga kudya chipatso, koma kusawakhulupirira Mawu a Mulungu. Kodi kudya chidutswa cha chipatso kukanawulula bwanji pomwepo kwa Adamu ndi Eva kuti iwowo anali amaliseche? Izo ndithudi sizikumveka mwanzeru. Kodi chipatso chiri ndi chochita chanji ndi umaliseche? Mneneri wa Mulungu anawulula chinsinsi ichi mosabisa.

Kodi angelo amene akunenedwa mu Chivumbulutso mutu wa 2 ndi 3 anali ndani? Maina awo akhoza kumveka modziwika.

Kodi okwera pa kavalo achinsinsi a Chivumbulutso 6 ndi ndani? Iwowo ali ndi chinthu chimodzi chofunikira kwambiri chofanana.

Kodi United States amatchulidwa mu Bukhu la Chivumbulutso?

Kodi 144,000 amene anapulumutsidwa mu mutu 7 ndi ndani?

Kodi hule wamkulu wa mutu wa 17 ndi ndani? Chimene iye ali ndi zinsinsi zonse izi zinaululidwa mu Uthenga wa mneneri wamphamvu uyu wotumidwa kuchokera kwa Mulungu.

Si kuti kokha zozizwitsa zosawerengeka zinkamutsatira munthu uyu, komanso zinsinsi zobisika mu Baibulo kudutsa mu mibadwo nazonso zinaululidwa mu Utumiki wake. Izo zinadzafika pomveka bwino kuti mneneri uyu anakwaniritsa Malemba ochuluka kuposa Malaki 4.

Chivumbulutso 10:7: Koma mu masiku a liwu la mngelo wachisanu ndi chiwiri, pamene iye adzayamba kuwomba, chinsinsi cha Mulungu chiyenera kutsirizika, monga iye ananenera kwa antchito ake aneneri.

Liwu likufuula kwa dziko lapansi kuti atuluke mu zipembedzo ndi kubwerera ku Mawu apachiyambi a Mulungu. Wina aliyense wa ife ali nawo mwayi womwewo umene Petro, Yakobo, ndi Yohane anali nawo. Ife tiri nawo mwayi woti tikhoza kuwerengedwa limodzi ndi osankhidwa apang’ono a Mulungu amene sanagwadire mabungwe achipembedzo a tsikuli.

Malemba Oyera amalemba miyoyo ndi zintchito za amuna amene ankayenda ndi Mulungu ndipo anali odzozedwa kwambiri ndi Mzimu Wake mwakuti iwo amalengeza PAKUTI ATERO AMBUYE, ndipo mawu awo ankatsimikiziridwa ndi zizindikiro ndi zodabwitsa zosalephera. Iwo anali aneneri a Mulungu, ndiponso Liwu la Mulungu kwa ka m’badwo kawoko.

Kodi nthawi zikusiyana tsopano ndi pamene Yesu anali kuno? Anali atsogoleri achipembedzo amene anamupachika Iye. Ophunzira anali apang’ono pakati pa kachitidwe kachipembedzo kakakulu. Iwo ankasekedwa, ankasereulidwa, ndipo potsiriza ankaphedwa chifukwa chotenga maimidwe otsutsa kachitidwe ka chipembedzo chachikulu. Ife tikhoza kusamaphedwa chifukwa cha zikhulupiriro zathu lero, koma ife ndithudi tikumazunzidwa. Monga Afarisi ndi Asaduki, iwo sangathe kuzikana zozizwitsa zimene zinkawutsatira utumiki wa M’bale Branham kotero mmalo mwake amathawira kumanyoza. Inu mukhoza kumva kuti iye anali mneneri wabodza, mtsogoleri wa mwambo, kapena zachipongwe zina. Kunena zoona, iye anali munthu wodzichepetsa wa Mulungu amene anaima mokhazikika kutsutsa kulamulira kosapindulitsa kumene zipembedzo ndi miyambo ziri nazo pa anthu a Mulungu. Iwo anamunena Yesu mwanjira yomweyo pamene Iye anaima motsutsa ziphunzitso zawo ndi miyambo.

Mulungu analemekeza kudzipereka kwa M’bale Branham kuti akhulupirire Mawu aliwonse mu Baibulo, ndipo Iye akugwiritsa ntchito utumiki wake kuti utsogolere miyoyo mamilioni kwa Yesu Khristu. Lero, Liwu la Mngelo Wachisanu ndi chiwiri likuwomba momveka monga momwe Ilo lakhala likuchitira. Pafupifupi anthu thuu milioni pa dziko lonse akukhulupirira Uthenga wa M’bale Branham. Awa akhoza kukhala apang’ono kwambiri mwa thuu bilioni amene amadzinenera za Chikhristu, koma ndi liti pamene anthu a Mulungu sanakhalepo apang’ono?

Ife tiri nawo oposa maulaliki ojambulidwa 1,200 amene ali ndi Liwu limene linaloseredwa kuti lidzabwera mu Chivumbulutso 10:7. Uliwonse wa maulaliki awa amamasula zinsinsi zochuluka za Mulungu. Liwu limenelo likhoza kupezeka kwa inu ngati inu mukulolela kuti mulimve Ilo.

 

CHISANKHOCHO NDI CHANU

Palibe mphindi imodzi yomwe ine ndimabweretsa uthenga kwa anthu kuti iwo azinditsata ine, kapena kujowina mpingo wanga, kapena kuyambitsa chiyanjano china ndi bungwe. Ine sindinayambe ndachitapo zimenezo ndipo sindichita zimenezo tsopano. Ine ndiribe chidwi ndi zinthu zimenezo, koma ndiri ndi chidwi ndi zinthu za Mulungu ndi anthuwo, ndipo ngati ine ndingathe kuchita chinthu chimodzi chokhacho ine ndikhala wokhutitsidwa. Chinthu chimodzi chimenecho ndi kuwona chitakhazikika chiyanjano chenicheni chauzimu pakati pa Mulungu ndi anthu, mmene anthu angakhale zolengedwa zatsopano mwa Khristu, odzazidwa ndi Mzimu Wake ndi kumakhala moyo molingana ndi Mawu Ake. Ine ndikhoza kuyitanira, kuchonderera ndi kuchenjeza onse kuti amve liwu Lake pa nthawi ino, ndi kuperekera miyoyo yanu kwathunthu kwa Iye, ngakhalenso monga ine ndikudalira mu mtima wanga kuti ine ndapereka zanga zonse kwa Iye. Mulungu akudalitseni inu, ndipo mulole kudza Kwake kukondweretse mtima wanu.”

M’busa William Marrion Branham

 

 

 

Mukafuna kuti mudziwe zambiri za utumiki wa M’busa William Marrion Branham ndi momwe mungapezere ma ulaliki ake, chonde mulembere ku:

THEMESSAGE.COM


kapena

Voice Of God Recordings, Malawi Office

P.O. Box 51453
Limbe, Malawi
www.branham.org