CHIYAMBI



“Pamene ine ndinkabadwa mu kanyumba kakang’ono ka ku Kentucky kumtunda uko, Mngelo wa Ambuye anadzabwera pa zenera ndipo anadzaima pamenepo. Apo panali Lawi la Moto.”

Kucha kwa tsiku kunali kukungoyamba kupyoza mdima wa mmwamba mozizira wa Epulo. Zenera limodzi, la matabwa linaima chitsegulireni kuti kuwala kwa mmawa kulowe mu kanyumba kakang’ono ka chipinda-chimodzi ako. Phwiti ataima pafupi ndi zeneralo ankawoneka kuti anali wosangalala kwambiri mmawa umenewu ndipo anali akuimba mokweza mawu kuchokera mmapapo ake. Mkati mwa kanyumbako, Charles Branham wachinyamata anaika manja ake mu ovololo yatsopano ndipo nkumamuyang’ana mkazi wake wa usinkhu wa zaka 15. “Ife timutchula dzina lake William,” anatero bambo ake.

Kudzera pa zenerapo panadzalowa Kuwala kwauzimu. Kuwalako kunadzayenda kudutsa mchipindamo ndipo kunadzafungatira pa bedi pamene mwanayo anali akungobadwa kumene. Uku kunali Kuwala komwe kuja kumene kunawatulutsa ana a Chihebri kuchokera ku Igupto. Iko kunali Kuwala komweko kumene kunakomana ndi Paulo panjira yake yaku Damasiko. Ndipo Iko kukanadzapitirira mpaka kukamutsogolera mwana wamng’ono uyu kuti akamuitanire Mkwatibwi wa Khristu kuchokera ku dziko lapansi. Kuwala kumeneko sikunali china koma Mngelo wa Ambuye, Lawi la Moto; ndipo apanso Ilo linali litawonekeranso kwa munthu.

Ndipo mmenemo, mu kanyumba kakang’ono ka zipika aka, mmawa umenewo pa Epulo 6, namwino anatsegula zenera kuti kuwala kuwalire mkati kuti Amama ndi Adadi awone momwe ine ndimawonekera. Kenako Kuwala pafupifupi usinkhu wa pilo kunabwera kukuzungulira kudutsa pa zenera. Iko kunadzazungulira pamene ine ndinali, ndipo kunadzatsikira pa bedipo. Angapo a anthu aku phiri anali ataima pamenepo. Iwo anali akulira.

Nyumba yaing’onoyo inali mmapiri a kummwera kwa Kentucky, pafupi ndi tawuni yaing’ono ya Burkesville. Tsiku lake linali Epulo 6, 1909. Mwanayo anali woyamba wa ana khumi amene akanati adzabadwe kwa a Charles ndi a Ella Branham.

Sipanatenge nthawi kudzafika pamene Mngelo wa Ambuye anadzamuchezeranso William Branham wamng’ono.

Pamene iye anali mwana, Mngelo poyamba analankhula ndi iye, kunena kuti iye akanadzakhala moyo wake pafupi ndi mzinda wotchedwa New Albany. Iye anakalowa mnyumba ndipo anakawauza amayi ake zimene zinali zitangochitika kumene. Monga mayi wina aliyense, iye sanalingalire mochuluka kwambiri za nkhaniyo ndipo anamugoneka iye kuti atontholetse misempha yake yanthete. Zaka ziwiri kenako, banja lake linasamukira ku Jeffersonville Indiana, mamailosi pang’ono chabe kuchokera ku mzinda wakummwera kwa Indiana wa New Albany.

Mngelo analankhulanso kwa mneneri wamng’onoyo zaka pang’ono kenako. Ilo linali tsiku labata la Seputembala lokhala ndi dzuwa lotentha likuwalira kudutsa masamba a mchilimwe. Mwanayo anali akutsimphina pamene iye anali atanyamula zidebe ziwiri za madzi akudutsa mkanjira. Chitsononkho cha chimanga chinali chitamangidwa kumsi kwa chala chake chovulala kuwopesera kuti icho chisagunde dothi. Iye anakhala pansi kuti apumule pa mthunzi wa mtengo wautali wa mthundu. Misonzi inali ikuyenderera kuchokera mmaso mwake pamene iye anali akulira chifukwa cha zodandaulitsa zake. Azimzake anali akusangalala ku malo owedza nsomba, ndipo iye anali wokakamizika kuti aziwatungira madzi abambo ake. Mwadzidzidzi, mphepo inayamba kuwomba mu mtengomo pamwamba pa iye. Iye anapukuta misonzi yake ndipo anaimirira ku mapazi ake. Iye anamva phokoso la masamba akuwomba mu mphepo…koma apo panalibe mphepo. Iye anayang’ana mmwamba, ndipo pafupifupi theka la mtengo wa mthunduwo, chinachake chinali kuwombetsa masamba owumawo.

Mwadzidzidzi Liwu linalankhula, “Usadzamwe kapena kusuta kapena kuipitsa thupi lako mwanjira iliyonse, idzakhalapo ntchito yoti iwe udzaichite pamene iwe uti udzakule.” Mnyamata wowopsyezedwa wa usinkhu wa zaka seveniyo anagwetsa zidebe zake ndipo anathamangira kwa amayi ake.

Monga mneneri Samuele, Mulungu apanso anali atalankhula kwa mwanayo.

Masabata pang’ono kenako, iye anali akusewera mabo ndi mng’ono wake. Kumverera kwachirendo kunabwera pa iye. Iye anayang’ana panja kudutsa Mtsinje wa Ohio ndipo anawona mulatho wokongola. Amuna sikisitini anagwa mpaka kufa pamene mulathowo unkawoloka mtsinje. Mneneri wamng’onoyo anali atawona masomphenya ake oyamba. Iye anawauza amayi ake, ndipo iwo analemba nkhani yakeyo. Zaka kenako, amuna 16 anagwa mpaka kufa pamene mulatho wa Msewu Wachiwiri mu Louisville, Kentucky unali kumangidwa pamwamba pa Mtsinje wa Ohio.

Ambuye anali akumusonyeza iye masomphenya a za mtsogolo. Ndipo monga aneneri a pambuyo pake, masomphenyawo sanalepherepo.