Yohane 14:12

Indetu, Indetu, Ine ndinena ndi inu, Iye amene akhulupirira pa ine, ntchito zimene Ine ndikuzichita iyenso azidzazichita; ndipo ntchito zazikulu kuposa Izi azidzazichita; chifukwa Ine ndikupita kwa Atate anga.

Marko 16:17-18

Ndipo zizindikiro Izi zidzawatsata iwo amene akhulupirira; Mu dzina langa iwo azidzatulutsa ziwanda; iwo azidzalankhula ndi malirime atsopano;

Iwo adzatola njoka; ndipo ngati iwo adzamwa kanthu kakupha kalikonse, iko sikadzawapweteka iwo; iwo adzaika manja awo pa odwala, ndipo iwo adzachira.


Tonse a ife tikhoza kutembenuza masamba a Baibulo ndi kuwona kuti Mulungu amachita zozizwitsa: Mose anagawaniza Nyanja Yofiira, Eliya anaitanitsa njala, Yesu anayenda pa madzi, ndipo ophunzira anachiritsa odwala.

Ziripo zochitika zozizwitsa zikwi zikwi zimene zalembedwa mu Baibulo. Ngati Mulungu amachitira umboni ndi zizindikiro ndi zodabwitsa, ndiye zozizwitsa Zake ziri kuti lero? Kodi Iye angathe kuchiza khansa monga Iye ankachizira khate mu Baibulo? Nanga bwanji EDZI kapena malungo? Kodi Iye angachitebe chozizwitsa? Inde, Mulungu akuchitabe zozizwitsa ndipo zizindikiro zimenezi zikuwatsatira iwo amene akukhulupirira.

Tsopano, taonani amzanga, talingalirani za Mfumu George yaku England, pamene iye anachiritsidwa ku zotupa zambiri, pamene ife tinamupempherera iye. Talingalirani za Florence Nightingale, (agogo ake aakazi, ndi amene anayambitsa Red Cross), anali kulemera pafupifupi mapaundi sikisite, anagonekedwa uko akufa ndi khansa ya mmatumbo mmimba, atagona pamenepo akufa. Nkhunda yaing’ono inawulukira mu tchire kumeneko ndipo Mzimu wa Mulungu unabwera ndipo unati, “PAKUTI ATERO AMBUYE, iye akhala moyo.” Ndipo iye akulemera mapaundi handiredi ndi fifite-faifi ali ndi thanzi langwiro.

Talingalirani za Congressman Upshaw omangokhala pa mpando ndi pa bedi kwa chaka ndi chaka, kwa zaka sikisite-sikisi. Ndipo basi mu kamphindi ka nthawi anadzuka ku mapazi ake, anathamanga kudutsa mnyumbamo, anakagwira zala zake zakuphazi, anali atachiritsidwa mwangwiro ndipo anali bwino bwino.

Tangoganizani za zikwi ndi zikwi za anthu amene achiritsidwa. Chifukwa chiyani ife tikumakhala pano mpakana kumafa? Tiyeni tichitepo chinachake za izo.

Mukhale ndi chikhulupiriro ngati inu mukudwala kapena ngati mukusowa. Baibulo limanena kuti Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi kwanthawizonse, kotero ngati Iye anali wokhoza kuchita chozizwitsa zaka thuu sauzande zapitazo, ndiye kuti Iyeyo ndi wokhoza kuchita chinthu chomwecho lero. Iye anatilonjeza ife kuti tachiritsidwa, ngati ife titangokhulupirira.

Congressman Upshaw

William D. Upshaw anagwira ntchito kwa zaka eyiti mu Nyumba ya Malamulo ya United States ndipo anadzaima nawo upurezidenti mu 1932. Ngozi ya ulimi inamupuwalitsa iye ali mwana, ndipo anakhala zaka 66 akuyendera ndodo kapena mu chikuku. Mu 1951, iye anachiritsidwa kwathunthu ndipo anadzayenda wangwiro moyo wake wonse.

 
Florence Nightingale

Florence Nightingale, wachibale wapatali kwa namwino wotchuka, anali ndi khansa ya mmimba yosachira. Iye anatumiza chithunzi ichi ngati pempho lomaliza la pemphero khansayo isanatsirize kutenga moyo wake. Monga mmene inu mukuwonera, iye anali pafupi kuti afe Ambuye Yesu asanamuchiritse iye mu 1950. Chithunzi chinacho chinajambulidwa pambuyo pa kuchiritsidwa kwake ndipo anachitumiza ngati umboni wakuti Mulungu akuchiritsabe odwala.


Tris Griffin

Tris Griffin anapita ku ofesi ya adokotala koyambirira kwa 2013 chifukwa cha kupweteka kwa nsana kumene iye ankawopa kuti kungakhale kubwereranso kwa vuto lake la khansa. Kujambula kunasonyeza “kung’ambika kwa msempha” mu mtima mwake, chimene chinapangitsa kuti madokotala amuyezebe mopitirira ndi kukonza kuti achitidwe opareshoni tsiku lotsatira lakelo. Mzere umene ukudutsa pa mtima mu chithunzichi ndi mn’galu wachidziwikire umene ungatanthauze imfa ya msanga ndi yotsimikizika ngati iwo utaphulika.

Tsiku lotsatira, okhulupirira atatha kumupempherera iye, madokotala anajambulanso kuti atsimikizire pamene panali mng’aluwo asanachite opareshoni. Nthawi iyi, chithunzi chinasonyeza mtima wathanzi kwathunthu. Atadodoma nazo, wochita opareshoniyo anawauza Akazi a Griffin, “Ine sindikudziwa zoti ndikuuzeni inu. Inu munali ndi kung’ambika kwa msempha, koma tsopano umboni wonse palibepo.” Iye anawasonyeza iwo zithunzi zonse asanapemphereredwe, ndipo kenako pambuyo pake. “Inu muli womasuka kupita, ndiponso powonjezera, palibeponso chisonyezo chakuti muli ndi khansa. Inu muli ndi thanzi langwiro.”

 

(kumanzere) Cholozera cha adokotala chikulozera pa msempha, umene uli malo akuda, ozungulira pakati pa chithunzichi. Mzere wogonawo umene ukudutsapowo ndi vuto la mu msempha, kapena “kung’ambika” kwa msempha, chimene chimasoweka opareshoni ya msangamsanga ndipo zimakhala kuti ukhoza kufa ngati utaphulika. (pamwamba) Kujambula kwachiwiri kunachitika tsiku lotsatira. Kung’ambikako kunasowa kwathunthu ndipo sikunabwererenso.

Zothandizira zake

Masalmo 103:2-3

Lemekeza YEHOVA, O moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse: Amene akhululukira mphulupulu zako zonse; amene achiritsa matenda ako onse;

Yesaya 53:5

Koma iye anavulazidwa chifukwa cha mphulupulu zathu, iye anatunduzidwa chifukwa cha kusayeruzika kwathu: chilango cha mtendere wathu chinali pa iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa.

Marko 16:17

Ndipo zizindikiro izi zidzawatsatira iwo amene akhulupirira; Mu dzina langa iwo azidzatulutsa ziwanda; iwo azidzalankhula ndi malirime atsopano;

Luka 17:6

Ndipo Ambuye anati, Ngati inu mukadakhala nacho chikhulupiriro ngati kambewu ka mpiru, mukadanena kwa mtengo uwu wa nkuyu, Uzulidwe kuchokera ku muzu, ndipo ukawokedwe mnyanja; ndipo iwo ukanakumverani inu.

Yohane 14:12

Indetu, indetu, ine ndinena kwa inu, Iye amene akhulupirira pa ine, ntchito zimene ine ndikuzichita iyenso azidzazichita ; ndipo ntchito zazikulu kuposa izi azidzazichita; chifukwa ine ndikupita kwa Atate anga.

I Atesalonika 1:5

Pakuti uthenga wathu sunadze kwa inu ndi mawu okha, komatunso mu mphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera; ndi kutsimikiza mochuluka monga mukudziwa kuti ife tinali amuna otani pakati panu chifukwa cha inu.

Ahebri 2:3-4

Kodi ife tidzapulumuka bwanji, tikanyalanyaza chipulumutso chachikuru chotere; chimene poyamba chinayamba kulankhulidwa ndi Ambuye, ndipo chinatsimikiziridwa kwa ife ndi iwo amene anamumva iye; Mulungunso anawachitira iwo umboni, ndi zizindikiro ndi zodabwitsa, ndi zozizwitsa zosiyanasiyana, ndi mphatso za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake?

Ahebri 13:8

Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi kwanthawizonse.

Yakobo 5:15

Ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzamupulumutsa wodwala, ndipo Ambuye adzamudzutsa iye; ndipo ngati iye wachita machimo, iwo adzakhululukidwa kwa iye.

I Petro 2:24

Amene anasenza machimo athu mwiniyekha mthupi lake lomwe pa mtengo, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo: ameneyo ndi mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.