Akatolika amakhulupirira kuti Mulungu adzaweruza dziko lapansi mogwirizana ndi ziphunzitso za mpingo wawo. Ngati Mulungu ati adzaweluze dziko lapansi monga mwa Mpingo wa Katolika, ndiye nanga bwanji Abaptisti? Kodi iwowo asochera? Nanga bwanji Ahindu ndi Asilamu? Mudzamudalira ndani pa za chipulumutso chanu chamuyaya? Mpingo wanu?



Masalmo 96:13

Pamaso pa AMBUYE: pakuti akudza, pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi: iye adzaweruza dziko ndi chilungamo, ndi anthu ndi choonadi chake.

Ziripo zipembedzo zikwi zikwi zosiyanasiyana mu dziko lero. Chipembedzo chirichonse chimadzudzula chimzake, komabe iwo onse amalonjeza chipulumutso mu chipembedzo chawocho. Kodi ife tingadziwe bwanji choti tichisankhe?

Ngati ife tisankha mpingo wa Katolika, ndiye kuti ife tavomereza kupembedzera kwa oyera, chimene sichikuposa kupembedza mafano. Baibulo limati, “Pakuti alipo Mulungu mmodzi, ndi mkhala pakati mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, mwamunayo Khristu Yesu;(I Timoteo 2:5). Wansembe amatchedwa “Bambo” chimene chinaletsedwa ndi Yesu mu Mateyu 23:9: “Ndipo musamutche munthu aliyense bambo pa dziko lapansi: pakuti alipo mmodzi yekha Atate wanu, yemwe ali kumwamba.” A Assemblies Of God amatiuza ife kuti kulankhula mu malirime ndi umboni woyambilira wa Mzimu Woyera, pamene Paulo anati, “Ngakhale ine ndingalankhule ndi malirime a anthu ndi a angelo, ndipo ngati ndiribe chikondi, ndikhala ngati mkuwa wolira, kapena nguli  yophokosera.(I Akorinto 13:1)

Pafupifupi zipembedzo zonse zimathamangira kutiuza ife kuti zinthu zambiri mu Baibulo zinatanthauziridwa molakwika, zinataika pomasulira, kapena siziri za dziko la lero. Kotero, kodi ife tiyenera kuti tizikhulupirira Baibulo kapena ziphunzitso za chipembedzo? Kodi Mulungu adzagwiritsa ntchito chiyani ngati muyezo wa chiweruzo?

Ngati ine nditawafunsa Achikatolika pano usikuuno, “Kodi inu mukuganiza kuti Mulungu adzaweruza dziko lapansi ndi chiyani?” Achikatolika anganene kuti, “Ndi Mpingo wa Katolika.” Chabwino, tsopano Mpingo wa Katolika wake uti? Tsopano iwo ali ndi Wachiroma, wa Greek Orthodox, ndi yambiri ya iwo. Udzakhala Mpingo wa Katolika wake uti? Achilutera amati, “Ndi ife,” ndiye inu Achibaptisti palibepo. Ndiyeno ngati ife titanena kuti, “Ndi Achibaptisti,” ndiye kuti inu Achipentekoste palibepo. Kotero pamenepo pangakhale chisokonezeko chachikulu, palibe amene angadziwe choti achite; kotero Iye sanalonjeze konse kuti adzaliweruza dziko pogwiritsa ntchito mpingo.

Iye analonjeza kuti adzaliweruza dziko ndi Khristu, ndipo Khristu ndi Mawu. Ndipo Baibulo ndi limene liti lidzaweruze dziko lapansi, amene ali Yesu Khristu yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse.


Zothandizira zake

Yohane 1:1

Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali ndi Mulungu, ndipo Mawu anali Mulungu.

Yohane 1:14

Ndipo Mawu anasandulika thupi, ndipo anadzakhala pakati pathu (ndipo ife tinawuwona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobalidwa yekhayo wa Atate,) wodzaza ndi chisomo ndi choonadi.

Yohane 5:22

Pakuti Atate saweruza munthu aliyense, koma anapereka kuweruza konse kwa Mwana:

Yohane 12:48

Iye amene andikana ine, ndi kusawalandira mawu anga, ali naye womuweruza iye: mawu amene ndalankhula, iwowa adzamuweruza iye tsiku lotsiriza.

Aefeso 1:5-7

Atatikonzeratu ife ku kulandilidwa ngati ana mwa Yesu Khristu kwa Iye yekha, monga umo kunakomera chifuniro chake, Ku kulemekeza kwa ulemerero wa chisomo chake, mmene iye watipanga ife kuti tilandilidwe mwa okondedwayo. Mwa amene tili ndi chiombolo kudzera mmagazi ake, chikhululukiro cha machimo, monga mwa kulemera kwa chisomo chake;

Aefeso 2:5-8

Ngakhale pamene tinali akufa mmachimo, watifulumizitsa limodzi ndi Khristu (muli opulumutsidwa ndi chisomo;) Ndipo anatiukitsa ife pamodzi, natikhazikitsa pamodzi mmalo a mwambamwamba mwa Khristu Yesu: Kuti akawonetsere mnyengo zirinkudza chuma choposa cha chisomo chake nkukoma mtima kwa pa ife mwa Khristu Yesu. Pakuti muli opulumutsidwa mwa chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro; ndipo ichi chosachokera kwa inu nokha: chiri mphatso ya Mulungu:

I Yohane 1:7

Koma ngati ife tiyenda mu kuwala, monga iye ali kuwala tiyanjana wina ndi mzake, ndipo mwazi wa Yesu Khristu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.

Chivumbulutso 22:18-19

Pakuti ndichitira umboni kwa munthu aliyense wakumva mawu a chinenero cha bukhu ili, Ngati munthu aliyense adzawonjezera pa zinthu izi, Mulungu adzawonjezera pa iye miliri yolembedwa mbukhumu: Ndipo ngati munthu aliyense adzachotsera mawu achinenero cha bukhu ili, Mulungu adzamuchotsera gawo lake mu bukhu la moyo, ndi kuchoka mu mzinda woyera, ndi ku zinthu zolembedwa mbukhu ili.