Malaki 4:1

Pakuti, taonani, likudza tsiku limene liti lidzawotche ngati ng’anjo...


Malaki 4:5-6

Taonani, ine ndidzakutumizirani inu Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi lowopsya la AMBUYE:
Ndipo iye adzatembenuza mtima wa atate kwa ana, ndi mtima wa ana kwa atate, kuwopa kuti ndingadze ndi kudzalikantha dziko ndi themberero.


Bukhu lotsiriza la Chipangano Chakale likulonjeza za chiwonongeko cha dziko lapansi. Koma chimalizirocho chisanafike, Eliya mneneri akunenedweratu kuti adzabwereranso ndi kudzawalozera Mesiya. Ena amanena kuti Yohane M’batizi anakwaniritsa ulosi umenewu.

Zaka thuu sauzande zapitazo, Ayuda ankayembekezera kuti Mesiya abwera. Iwo ankadziwa kuti Malaki analosera kuti munthu wokhala ndi mzimu wa Eliya akanadzawalozera Mesiya kwa iwo. Koma pamene Yohane M’batizi anabwera, iye sanali chimene iwo ankayembekezera kuti Eliya akanadzakhala. Pamene anamufunsa Yesu kuti bwanji Eliya sanadze poyamba, Iye anawawuza iwo mwachimvekere kuti Yohane anali kukwaniritsa kwa ulosi umenewo: “Ndipo ngati inu mungamulandire iye, uyu ndiye Elias, amene anali woti adze.” (Elias ndi kulemba kwa Chigriki kwa dzina la Chihebri la Eliya.)

Linali gulu la pang’ono lokha la anthu limene linalandira vumbulutso ili. Kwa atsogoleri ambiri achipembedzo, Yohane sanali china koma wotsutsa wotengeka wa mabungwe awo. Sikuti sanangowuzindikira kokha mzimu wa Eliya, koma zoipitsitsa zake, iwo anakuphonyanso Kudza kwa Khristu.

Kotero kodi Yohane M’batizi anakwaniritsa uneneri wa Malaki? Osati kwathunthu.

Poyamba pomwe, dziko “silinawotchedwe ngati ng’anjo” mpaka pano, kotero ife tikudziwa kuti ndithudi gawo la Malaki 4 liri lakuti lidzachitikabe. Gawo lina la Lemba limene silinakwaniritsidwe ndi Yohane linali, “adzatembenuza mtima wa ana kwa atate awo.” Ndipo, Yesu, Mwiniwake, analosera kuti Eliya adzadza (mtsogolo) nadzabwezeretsa zinthu zonse. (Mateyu 17:11)

Choncho ife tiziyembekezera Eliya kusanafike Kudza Kwachiwiri kwa Khristu!

Tsopano, mu tsiku lamakono lino, ndiyo nthawi ya Kudza Kwachiwiri kwa Ambuye Yesu. Apanso, ife tikulonjezedwa kuti mzimu wa Eliya udzamulozera Iye kwa ife molingana ndi Malaki 4. Koma ndi gulu lanji la anthu limene liti lidzamuzindikire Eliya pamene iye azidzabwera? Okhawo amene akumuyembekezera iye.

Mawu awa a Ambuye wathu ndi Mpulumutsi amakumbukiridwa pamene ife tilingalira za ulosi wa Malaki wa mmaora otsekera ano a nthawi.

Koma ine ndinena ndi inu, Kuti Eliya anadza kale, ndipo iwo sanamudziwe iye ayi... Mateyu 17:12

Nanga bwanji ngati ife titaphonya kubwera kwa Eliya uku? Kodi ndiye kuti ife tidzaphonya Kubwera Kwachiwiri kwa Khristu, monga alembi ndi Afarisi anaphonyera Kudza kwake Koyamba chifukwa chakuti iwo sanamuzindikire Yohane M’batizi?

 

 

 

 

Zothandizira zake

II Mafumu 2:15

Ndipo pamene ana a aneneri okhala ku Yeriko anamuwona iye, iwo anati, Mzimu wa Eliya watera pa Elisha. Ndipo anadza kukomana naye, nadziweramitsa pansi kumaso kwake.

Yesaya 40:3-4

Liwu la iye wofuula mu chipululu, Konzani inu njira ya Ambuye, mukonze mchipululu msewu wawukulu wa Mulungu woti see. Chigwa chirichonse chidzadzazidwa, ndipo phiri lirilonse ndi chitunda chirichonse zidzachepetsedwa: ndipo zokhota zidzawongoledwa, ndipo malo okumbika adzasalazidwa: [Yohane M’batizi]

Malaki 3:1

Taonani, ine ndidzakutumizirani inu mtumiki [Yohane M’batizi], ndipo iye adzakonzeratu njira pamaso panga: ndipo Ambuye, amene inu mukumfuna, adzadza ku kachisi wake modzidzimutsa, ngakhale mtumiki wa phangano, amene inu mukondwera naye: taonani, iye adzadza, atero Ambuye wamakamu.

Malaki 4:1-6

Pakuti, taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng’anjo [sizinachitikebe]; ndipo onse akudzikuza, eya, ndi onse akuchita choipa, adzakhala ngati chiputu: ndi tsiku lirinkudza lidzawayatsa iwo, ati Ambuye wamakamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.

Koma inu akuwopa dzina langa Dzuwa la chilungamo lidzakuturukirani muli kuchiritsa mmapiko mwake; ndipo mudzaturuka, ndi kutumphatumpha ngati ana a ng’ombe onenepa.

Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa ku mapazi anu tsiku ndidzaikalo, ati Ambuye wa makamu.

Kumbukirani inu chilamulo cha Mose mtumiki wanga, chimene ndinamlamuliracho mu Horebu chikhale cha Israeli yense, ndi malemba ndi maweruzo.

Taonani, ine ndidzakutumizirani inu Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikuru ndi lowopsya la Ambuye:

Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana [Yohane M’batizi], ndi mtima wa ana kwa atate awo [Eliya wa makono ano], kuti ndisafike ndi kukantha dziko liwonongeke konse.

Mateyu 11:10

Pakuti uyu ndi iyeyo, amene kunalembedwa za iye, Taonani, ine ndituma mtumiki wanga pamaso panu, amene adzakonzekeretse njira yanu patsogolo panu. [Malaki 3:1, Yohane M’batizi]

Mateyu 11:14

Ndipo ngati inu mumulandira iye, uyu ndiye Elias, amene amati akudza. [Yohane M’batizi]

Mateyu 17:11-12

Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Eliya ndithudi akudzatu, nadzabwezeretsa zinthu zonse. [Eliya wa makono ano] Koma Ine ndinena ndi inu, Kuti Eliya anadza kale, ndipo iwo sanamudziwe iye, koma anamchitira iye zonse zimene anazifuna iwo. Chomwechonso Mwana wa munthu adzazunzidwa ndi iwo. [Yohane M’batizi]

Luka 1:17

Ndipo iye adzamtsogolera iye mu mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kukatembenuzira mitima ya atate kwa ana awo, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka. [Yohane Mbatizi]