ZAKA ZA KUUBWANA - Continued



Munayamba kuchita mdima mu chipinda cha ku chipatalacho, ngati kuti umo munali mu nkhalango mowirira. Ine ndimakhoza kumva mphepo ikuwomba kudutsa mmasamba, komabe izo zimawoneka kuti kunali kutali ku nkhalango. Inu mwinamwake munamvapo kuwomba kwa mphepo ikukupiza masamba, ikubwera pafupi ndi pafupi kwa inu. Ine ndinaganiza, “Chabwino, iyi ndi imfa ikubwera kuti idzanditenge ine.” O! moyo wanga unali woti ukukakomana naye Mulungu, ine ndinayesera kuti ndipemphere koma sizinatheke ayi.

Mphepoyo inayamba kuyandikira, ndi kumaphokosera. Masamba amasokosa ndipo zonse mwakamodzi, ine ndinali nditapita.

Zinawoneka pamenepo kuti ine ndinali nditabwereranso kachiwiri kukakhala mnyamata wamng’ono wosavala nsapato, nditaimirira mu msewu umenewo pansi pa mtengo womwewo. Ine ndinamva Liwu lomwe lija limene linati, “Usadzamwe kapena kusuta.” Ndipo masamba amene ine ndinawamva anali omwe aja amene ankawomba mu mtengo womwe uja tsiku lijali.

Koma nthawi iyi Liwu linati, “Ine ndinakuitana iwe ndipo iwe sunapite ayi.” Ilo linabwereza katatu.

Ndiye ine ndinati, “Ambuye, ngati ameneyo muli Inu, mundirole ine ndibwererenso ku dziko lapansi ndipo ine ndikalalikira Uthenga Wanu kuyambira pa denga la nyumba ndi mokhotera misewu. Ine ndikamuuza aliyense za iwo!”

Pamene masomphenya awa anadutsa, ine ndinadzapeza kuti ine ndinali ndisanapezebe bwino. Wondichita opareshoni wangayo anali akadali mu chipindacho. Iye anabwera ndipo anadzandiyang’ana ine ndipo anadabwitsidwa. Iye ankawoneka ngati kuti amaganiza kuti ine ndifa, ndiye iye anati, “Ine sindine munthu wopita ku tchalitchi, ntchito yanga ndachita bwino kwambiri, koma ine ndikudziwa Mulungu wadzamuchezera mnyamata uyu.” Chifukwa chimene iye ananenera zimenezo, ine sindikudziwa. Palibe aliyense ananenapo chirichonse cha zimenezo. Ngati ine ndikanati ndinkadziwa pa nthawi imeneyo zimene ine ndikuzidziwa tsopano, ine ndikanadzuka pa bedi imeneyo ndikufuula Matamando kwa Dzina Lake.

Patatha masiku pang’ono ine ndinalolezedwa kuti ndibwerere kwathu koma ine ndinali ndikudwalabe ndipo ndinakakamizidwa kuti ndizivala magalasi mmaso mwanga chifukwa cha kujejema kwa maso. Mutu wanga unkagwedera ine ndikayang’ana pa chirichonse kwa mphindi.

Ine ndinawuyamba kuti ndikamufunefune ndi kumpeza Mulungu. Ine ndinapita tchalitchi ndi tchalitchi, kuyesera kuti ndipeze malo ena kumene kunali kuitanira kwa pa guwa kwa kachitidwe-kachikale. Gawo lachisoni linali lakuti ine sindimatha kupeza aliwonse.

Ine ndinanena kuti ngati ine ndidzakhale konse Mkhristu, ine ndidzakhaladi weniweni. Mtumiki yemwe anandimva ine ndikunena zimenezo anati, “Tsopano Billy mnyamata, iwe ukulowa mu zotengeka.” Ine ndinati ngati ine ndidzachipeze konse chipembedzo, ine ndikufuna kuti ndizidzachimverera icho pamene icho chikubwera, chimodzimodzi monga ophunzira ankachitira.

O litamandike Dzina Lake. Ine ndinadzachipeza chipembedzo kenako ndipo ine ndikadali nachobe icho, ndipo mothandizidwa ndi iyeyo, ine ndikhala ndikuchisunga icho nthawizonse.

Usiku wina ine ndinali ndi njala kwambiri yofuna Mulungu ndi chondichitikira chenicheni mwakuti ine ndinapita ku shedi yakale kuseri kwa nyumba ndi kukayesera kuti ndipemphere. Ine sindinkadziwa kuti ndipemphera chotani nthawi imeneyo kotero ine ndinangoyamba kulankhula naye Iye chimodzimodzi monga ine ndingalankhulire ndi aliyense. Mwadzidzidzi panabwera Kuwala mu shedimo ndipo iko kunadzapanga mtanda ndipo Liwu kuchokera pa mtandapo linalankhula kwa ine mu chinenero chimene ine sindinathe kumva. Kenako ilo linachokapo. Ine ndinali kakasi. Pamene ine ndinatsitsimuka ine ndinapempheranso, “Ambuye ngati ameneyo muli Inu, chonde mubwere ndipo mudzalankhulenso ndi ine kachiwiri.” Ine ndinakhala ndikuwerenga Baibulo langa chibwerereni kunyumba kuchokera ku chipatala ndipo ine ndinali nditawerenga mu Yohane 4, “Okondedwa, musakhulupirire mizimu iliyonse, koma muyiyese iyo ngati iyo ili ya Mulungu.”

Ine ndinadziwa kuti mzimu unali utawonekera kwa ine ndipo pamene ine ndimapemphera iwo unadzawonekeranso kachiwiri. Ndiye izo zinawoneka kwa ine kuti panali zikwi za mapaundi zimene zinachotsedwa kuchokera mmoyo mwanga. Ine ndinalumpha mmwamba ndipo ndinathamangira kunyumba ndipo zimakhala ngati kuti ine ndimathamanga mmalere.

Amayi anandifunsa, “Bill, chachitika ndi chiyani kwa iwe?” Ine ndinayankha, “ine sindikudziwa koma ndithudi ine ndikumverera bwino ndipo ndapepukidwa.” Ine sindinakhoze kukhala mnyumbamo aponso. Ine ndinapita panja ndi kumakathamanga.

Ine ndinadziwa pamenepo kuti ngati Mulungu akufuna kuti ine ndizikalalikira Iye andichiritsa ine. Kotero ine ndinapita ku tchalitchi chimene chinkakhulupirira mu kudzoza mafuta ndipo ine ndinakachiritsidwa nthawi yomweyo. Ine ndinawona pamenepo kuti ophunzira anali nacho chinachake chimene azitumiki ambiri alibe lero. Ophunzira ankabatizidwa ndi Mzimu Woyera ndipo amathanso kuchiritsa odwala ndi kuchita zozizwitsa zamphamvu mu Dzina Lake. Kotero ine ndinayamba kupempherera ubatizo wa Mzimu Woyera ndipo ndinawulandira iwo.

Tsiku lina pafupifupi miyezi sikisi kenako, Mulungu anadzandipatsa ine chokhumba cha mtima wanga. Iye analankhula ndi ine mu Kuwala kwakukulu, kumandiuza ine kuti ndipite ndikalalikire ndi kukawapempherera odwala ndipo Iye akanadzamawachiritsa iwo mosalabadira kuti iwowo anali ndi matenda anji. Ine ndinayamba kumalalikira ndi kumachita zimene Iye anandiuza ine kuti ndichite. O mzanga, ine sindingayambe kukuuzani inu zonse zimene zachitika: Maso akhungu atseguka. Olumala ayenda. Makhansa achiritsidwa, ndipo mitundu yonse ya zozizwitsa yachitika.

Tsiku lina pa tsinde la Spring Street, Jeffersonville, Indiana, chitatha chitsitsimutso cha masabata awiri, ine ndinali kubatiza anthu 130. Linali tsiku la mu Ogasiti lotentha ndipo apo panali pafupifupi anthu 3,000 amene anali pamenepo. Ine ndinali pafupi kuti ndimubatize munthu wa chi 17 pamene zonse mwadzidzidzi ine ndinamva Liwu laling’ono, la chiyeziyezi lija aponso ndipo ilo linati, “Yang’ana mmwamba.” Mu mlengalenga munali ngati mkuwa pa tsiku lotentha ilo la mu Ogasiti. Ife tinali tisanakhale ndi mvula iliyonse kwa pafupi masabata atatu. Ine ndinamva Liwu aponso, ndiyeno kenanso nthawi yachitatu ilo linati “Yang’ana mmwamba.”

Ine ndinayang’ana mmwamba ndipo apo panabwera kuchokera mu mlengalenga nyenyezi yaikulu yowala, imene ine ndinkaiwona nthawi zambiri mmbuyo koma kuti ine ndinali ndisanakuuzeni inu za iyo. Nthawi zambiri ine ndawawuzapo anthu za kuwonekera kwa iyo ndipo iwo amangoseka ndi kumati, “Bill, iwe ukungolingalira zimenezo. Kapena mwinamwake iwe umalota.” Koma Mulungu alemekezeke, nthawi iyi Iye anali akudziwonetsera Iyemwini mowonekera kwa onse, chifukwa iyo inafika pafupi kwambiri kwa ine mwakuti ine ndinalephera kuti ndilankhule. Patadutsa mphindi pang’ono ine ndinafuula ndipo anthu ambiri anayang’ana mmwamba ndipo anaiwona nyenyeziyo ili pamwamba pa ine. Ena anakomoka pamene ena anafuula ndipo ena anathawa. Ndiye nyenyeziyo inabwereranso mu mlengalenga ndipo malo amene iyo inali itachokapo panali pafupifupi mapazi fifitini monsemonse ndipo malo awa anakhala akumasunthabe ndi kumatakasika kapena ngati kuti mafunde akugudubuzika. Panali patawumbika pa malo aang’ono amenewa mtambo woyera ndipo nyenyeziyo inalandiridwa mu ka mtambo kakang’ono aka.

Monga Yohane M’batizi, mneneriyo anatsimikiziridwa mmadzi a Ubatizo.