Mmunda wa Edeni, serpenti “anamunyenga” Eva kuti adye chipatso. Iye anadya ndipo kenako anakamupatsa icho mwamuna wake, chimene chinawapangitsa iwo kuti azindikire kuti anali amaliseche. Ndi njoka ya mtundu wanji imene ingathe kulankhula, ndipo chipatso chiri ndi chochita chanji pa kukhala amaliseche?Genesis 3:1

Tsopano serpenti anali wochenjera kwambiri kuposa zamoyo zonse za mmunda zimene AMBUYE Mulungu anazipanga. Ndipo iye anati kwa mkaziyo, Eya, Mulungu anati, Inu musadzadye za mtengo uliwonse wa mmundamo?

Genesis 3:6-7

Ndipo pamene mkaziyo anawona kuti mtengowo unali wabwino kuwudya, ndipo kuti unali wokondweretsa mmaso, ndi mtengo wolakalakika wakupatsa nzeru anatenga zipatso zake, ndipo anadya, ndipo anapatsanso mwamuna wake limodzi ndi iye; ndipo iye anadya.

Ndipo anatseguka maso awo a onse awiri, ndipo iwo anadziwa kuti anali amaliseche; ndipo anasoka masamba a mkuyu limodzi, ndipo anadzipangira okha matewera.

Genesis 3:14-15

Ndipo AMBUYE Mulungu anati kwa serpenti, Chifukwa iwe wachita ichi, ndiwe wotembereredwa mwa zinyama zonse, ndi zamoyo zonse za kuthengo; uziyenda ndi pamimba pako, ndipo uzidya fumbi masiku onse a moyo wako:

Ndipo ine ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendene chake.

Ili ndi tchimo loyamba kulembedwa mu Baibulo. Chothyathyalika kwambiri mwa zamoyo zonse, serpenti, “anamunyenga” Eva kuti akadye chidutswa cha chipatso choletsedwa. Iye anadya icho ndipo kenako anamupatsa icho mwamuna wake, chimene chinapangitsa kuti iwo azindikire kuti iwo anali amaliseche.

Mafunso achidziwikireni ndi akuti: Kodi njoka imatha bwanji kulankhula? Kodi apulo ingakhale ndi chochita chanji ndi kukhala wamaliseche? Ndi, kodi mbewu ya serpenti ikubweramo pati mu zonse izi?

Baibulo limati serpenti anali “wochenjera” kwambiri mwa zamoyo zonse. Iye anali ngati munthu, mwakuti iye amakhoza kuyenda, kulankhula, ndipo ngakhale kukhala ndi kulankhulana kwa luntha. Iye atatha kumunyenga mkazi wa Adamu, Mulungu anamutemberera iye kuti akhale njoka, koma osati asanachite kuwonongako ndipo mbewu nkubzalidwa.

Baibulo limanena mu Genesis 3:15 kuti serpenti anali ndi mbewu, ndipo Mulungu anaika udani pakati pa mbewu ziwirizo. Chachidziwikireni, mbewu ya serpenti inasakanizikirana ndi mbewu yachirengedwe ya Eva kusanachitike kusiyanako. Kodi zonsezo zingakhale bwanji zotsatira zakudya apulo? Ndiye, ndime pang’ono kenako, “Adamu anatchula dzina la mkazi wake Eva; chifukwa iye anali mayi wa zamoyo zonse.” Zindikirani kuti ilo silimanena kuti Adamu anali atate wa amoyo onse.

Ziripo “zipatso” zosiyana mu Baibulo. Ndithudi, chiripo chipatso chenicheni, monga apulo, chimene chimamera ndipo chimadyedwa ngati chakudya. Chiriponso chipatso chimene chimanenedwa ngati ntchito zathu, kaya izo ndi ntchito zathupi monga ngati kulima ndi kuchita malonda, kapena ntchito zauzimu monga ngati kuchita zozizwitsa ndi kulalikira Uthenga. Ndiye, chiriponso chipatso cha mchiberekero, chimene chimanenedwa kuti ndi kutenga pakati ndi kubereka mwana.

Kodi kudya chipatso chenicheni kungawapatse Adamu ndi Eva kuzindikira kuti iwowo anali amaliseche? Kapena, kodi iko kungatenge ubale wathupi wa pakati pa mwamuna ndi mkazi kuti iwo azindikire chifukwa chimene iwo ayenera kuphimbira ziwalo zina za matupi awo?

Chinachitika ndi chiani kwenikweni tsiku limene lija mMunda chimene chinapangitsa mtundu wonse wa anthu kuti ugwe?

Monga Mbewu ya mkazi inali kwenikweni Mulungu kudzibala Yekha mu thupi la munthu, kotero mbewu ya serpenti ndiyo njira yeniyeni imene Satana anayipeza kuti iye anali wokhoza kutsegulira chitseko kwa iyemwini kulowa mu mtundu wa anthu. Kunali kosatheka kwa Satana (pakuti iye ali chabe CHOLENGEDWA chokhalapo chauzimu) kuti adzibale yekha mu chikhalidwe chomwe Mulungu anadzibalira Yekha, kotero nkhani ya Genesis imatiwuza momwe iye anaperekera mbewu yake nayambitsa kapena kudzilowetsa yekha mu mtundu wa anthu. Ndiponso mukumbukire kuti Satana akutchedwa “serpenti.” Iyo ili mbewu yake kapena kulowetsa mwa mtundu wa anthu kumene ife tikukunena.

Adamu asanakhale ndi kudziwa kwa umunthu wa Eva, serpenti anali ndi kudziwa uko patsogolo pa iye. Ndipo mmodzi uyo wobadwa kwa iyo anali Kaini. Kaini anali wa (wobadwa wa, wake wa) uyo “Mmodzi Woyipayo,”

I Yohane 3:12

…Choonadi cha nkhaniyo ndi chakuti Eva anali nawo mmimba mwake ana AWIRI amuna (mapasa) kuchokera kukupatsidwa mimba KOSIYANA. Iye anali kunyamula mapasa, ndi pakati pa Kaini nthawi ina yotsogolera kwa apo pa Abele.


Zothandizira zake

Genesis 3:6-7

Ndipo pamene mkaziyo anawona kuti mtengowo unali wabwino kuwudya, ndipo kuti unali wokondweretsa mmaso, ndi mtengo wolakalakika wakupatsa nzeru, anatenga zipatso zake, ndipo anadya, ndipo anakamupatsanso mwamuna wake limodzi ndi iye; ndipo iye anadya.

Ndipo anatseguka maso awo a onse awiri, ndipo iwo anadziwa kuti anali amaliseche; ndipo anasoka masamba a mkuyu, nadzipangira matewera.

[Kodi iwo anadziwa bwanji kuti iwo anali maliseche chifukwa cha kudya chipatso?]

Genesis 3:13-15

Ndipo AMBUYE Mulungu anati kwa mkaziyo, Ndi chiyani ichi chimene iwe wachita? Ndipo mkaziyo anati, Serpenti wandinyenga ine, ndipo ine ndadya.

Ndipo AMBUYE Mulungu anati kwa serpenti, Chifukwa iwe wachita ichi, ndiwe wotembereredwa mwa zinyama zonse ndi zamoyo zonse za kuthengo; uziyenda ndi pamimba pako, ndipo uzidya fumbi masiku onse a moyo wako:

Ndipo ine ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako ndipo iwe udzalalira chitendene chake.

[Serpenti anali nayo mbewu. Mwachidziwikire, apa sakunena za njoka.]

Genesis 3:20

Ndipo Adamu anatchula dzina la mkazi wake Eva; chifukwa iye anali mayi wa amoyo onse.

[Nchifukwa chiyani Adamu sakutchedwa bambo wa amoyo onse?]

Genesis 4:1-2

Ndipo Adamu anamudziwa mkazi wake Eva; ndipo iye anakhala ndi pakati, ndipo anabala Kaini, ndipo anati, ine ndalandira munthu kuchokera kwa AMBUYE. Ndipo iye kachiwiri anabala m’bale wake Abele. Ndipo Abele anali woweta nkhosa, koma Kaini anali wolima mu nthaka.

[Moyo wonse umabwera kuchokera kwa Mulungu, kaya kutenga mimba movomerezeka kapena mosavomerezeka. Satana sangathe kulenga moyo.]

Luka 3:38

Amene anali mwana wa Enosi, amene anali mwana wa Seti, amene anali mwana wa Adamu, amene anali mwana wa Mulungu.

[Alikuti mwana woyamba kubadwa Kaini mu mndamnda wa Adamu?]

I Yohane 3:12

Osati monga Kaini, amene anali wa woipayo, ndipo anamupha m’bale wake. Ndipo kodi iye anamupheranji iye? Chifukwa chakuti ntchito zake zomwe zinali zoipa, ndi za m’bale wake zolungama.

[Mulungu anamulenga Adamu mmawonekedwe Ake omwe. Kodi kuipa kwa Kaini kunachokera kuti, ndipo kodi kulungama kwa Abele kunachokera kuti? Makhalidwe awo anachokera kwa makolo awo.]

Yuda 1:14

Ndipo Enoki nayenso, wachisanu ndi chiwiri kuchokera kwa Adamu, analosera za izi, pakunena kuti, Taonani, Ambuye akudza ndi zikwi makumi za oyera ake,