Yohane 5:28-29

Musazizwe ndi ichi: pakuti ora likudza, limene onse amene ali mmanda adzamva liwu lake, Ndipo adzaturukira; iwo amene anachita zabwino kuukira ku moyo ndipo iwo amene anachita zoipa kuukira ku chiwonongeko.Likubwera tsiku limene wina aliyense wa ife, kaya ndi Mkhristu kapena ayi, adzapeza kwenikweni chimene chiri kuseri kwa katani la nthawi. Baibulo limalonjeza Moyo Wamuyaya kwa ena, ndi kwa ena, kwalonjezedwa chiwonongeko. Munthu aliyense kudutsa mu mbiriyakale ndithudi wadzifunsapo yekha, “Kodi ine chidzandichitikire ndi chiyani ndikadzafa?”

Kale lisanakhalepo konse Baibulo lowerenga, mneneri Yobu ankayang’ana pa chirengedwe. Iye ankanena za chiyembekezo cha mtengo, momwe iwo umadulidwa ndi kufa, komabe kudzera mu kafungo ka madzi, iwo umaphukiranso ku moyo ndipo iwo umaturutsanso mphukira zatsopano. Yobu ankadziwa kuti munthu, chimodzimodzi ngati mtengo, angadzakhoze kuwukanso ku moyo:

Kodi munthu akafa, adzakhalanso ndi moyo? masiku onse a nthawi yanga yoyikika ine ndidzadikirira, mpaka kudzafike kusandulika kwanga.

Inu mudzaitana, ndipo ndidzakuyankhani: inu mudzakhala nacho chikhumbo pa ntchito ya manja anu.

Pakuti tsopano inu muwerenga moponda mwanga: kodi inu simuyang’anitsa tchimo langa? (Yobu 14:14-16)

Yobu akhoza kukhala kuti analibe Baibulo lakuti aziwerengapo, koma iye ankadziwa kuti tsiku lina Mulungu adzamuukitsa iye kuchokera mmanda pamene Muwomboli wa mtundu wa anthu adzatulukire.

O akadalembedwa mawu anga tsopano! o iwo akadasindikizidwa m’bukhu!

Iwo akadazokotedwa pa thanthwe ndi chozokotera chachitsulo ndi kuthira ntovu kwa nthawizonse.

Pakuti ine ndikudziwa kuti muomboli wanga ali ndi moyo, ndipo kuti adzawuka potsiriza pa fumbi:

Ndipo angakhale mphutsi za khungu langa zitaliwononga thupi ili, komabe mu thupi langa ndidzamuwona Mulungu: (Yobu 19:23-26)

Mneneri anali kulankhula za Ambuye Yesu ndi chiukitsiro cha anthu Ake. Mwa vumbulutso Yobu ankadziwa kuti ngakhale matupi athu atafoteratu, Yesu adzawubwezeretsanso mnofu wathu. Ndipo ndi maso athu, ife tidzawona Kubwera Kwake. Anthu onse a Mulungu akuyembekeza kuti adzaliwone tsiku laulemerero ilo.

Komabe, chimodzimodzi basi monga Mulungu alipo, mdierekezi nayenso alipo; ndipo monga timatsimikiza kuti Kumwamba kulipo, gehena nayenso alipo. Phindu lake ndi lalikulu kuposa momwe ife tikuganizira. Mtumwi Paulo ananena kuti, “Diso silinaziwone, ndi khutu silinazimva, sizinalowenso mu mtima wa munthu, zinthu zimene Mulungu wawakonzera iwo amene amamukonda iye.” (I Cor. 2:9)

Malingaliro athu sangathe kumvetsa momwe Kumwamba kwakukulu kuti kudzakhalire, ndipo iwonso sangathe kumvetsa zowopsya za ku gehena. Yesu anatiuza ife kuti ku gehena ndi koyipa kwambiri mwakuti zikanakhala zabwino tikanadula chiwalo cha thupi lathu kuposa kuti tikapite ku malo owopsya amenewo.

Ndipo ngati dzanja lako likulakwitsa iwe, ulidule ilo: nkwabwino kwa iwe kulowa mmoyo wolumala, koposa kukhala ndi manja ako awiri ndi kulowa mu gehena, mu moto wosazimitsika: (Marko 9:43)

Kotero ndi ndani ati adzapite Kumwamba? Ndipo ndi ndani ati adzapite ku gehena? Ilo ndi lingaliro lomvetsa chisoni, koma Yesu ananena kuti anthu ambiri sadzalandira mphotho imene Iye akufuna kuti adzapereke: Lowani inu pa chipata chopapatiza: pakuti chipata chiri chachikulu, ndi njira ili yotakata, yakumuka nayo kuchiwonongeko, ndipo adzakhalako ambiri akulowa pa icho: Pakuti chipata chiri chopapatiza, ndipo njirayo ndi yaing’ono, yakumuka nayo ku moyo, ndipo adzakhalapo apang’ono amene ati adzaipeze iyo. (Mateyu 7:13-14)

Yesu ananenanso, “Si yense wakunena kwa ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu ufumu wa kumwamba; koma iye wakuchita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba. Ambiri adzati kwa ine tsiku limenelo, Ambuye, Ambuye, sitinanenera mawu mu dzina lanu? ndipo mu dzina lanunso kuturutsa ziwanda? ndipo mu dzina lanunso sitinachita ntchito zambiri zodabwitsa? Ndipo pamenepo ndidzafuulira iwo, ine sindinakudziwani inu: chokani kwa ine, inu akuchita kusayeruzika.” (Mateyu 7:21-23)

Si chifukwa chakuti munthuyo amadzinenera Chikhristu ndiye kuti iyeyo ndi wopulumutsidwa. Kotero, ili ndi funso lachidziwikireni mmalingaliro mwathu: Kodi ine ndingalandire bwanji Moyo Wamuyaya? Yesu anatipatsa ife yankho lophweka kwambiri: Indetu, indetu, ine ndinena kwa inu, Iye amene amva mawu anga, ndi kukhulupirira pa iye amene anandituma ine, ali nawo moyo wosatha, ndipo sadzafika ku chiwonongeko; koma wadutsa ku imfa ndipo wapita ku moyo. (Yohane 5:24)

Kuipa kwake, ndi kwakuti alipo anthu apang’ono kwambiri pa dziko lapansi lero amene amakhala ololera kutenga nthawi yawo pa masiku awo otangwanika kuti akamvetsere Mawu a Mulungu. Ndipo aliponso apang’ono amene amakhulupirira Mawu pamene iwo awamva mawuwo.

Matchalitchi amatiuza ife kuti tizikhala anthu abwino, tiziganiza zabwino, osamanama, kunyengeza, kapena kuba, ndipo tikatero ife tidzapita Kumwamba. Iwo sakudziwa kuti ku gehena kukadzadza ndi anthu amene amawoneka kuti amakhala miyoyo yabwino. Chenicheni chake ndi chakuti ife sitidzapita Kumwamba chifukwa cha ntchito zathu zolungama kapena chifukwa chakuti ndife membala wa mpingo wina wake. Ilipo njira imodzi yokha yopitira ku Moyo Wamuyaya, ndipo imeneyo ndi kudzera mwa Yesu Khristu. Iye anatilangiza ife kuti tiyenera KUKHULUPIRIRA Mawu Ake, amene ali Baibulo. Ngati sichoncho, ndiye ife tingapulumutsidwe bwanji?

Pamene tsiku la chiweruzo lidzakufikirani inu, kodi inu mudzamva, “Bwerani, inu odalitsika a Atate anga, lowani mu ufumu wokonzedwera inu asanakhazikitsidwe maziko a dziko lapansi,” (Mateyu 25:34) kapena kodi inu mudzamva, “Chokani kwa ine, inu otembereredwa, kaloweni ku moto wa nthawi zonse, wokonzedwera mdierekezi ndi angelo ake”? (Mateyu 25:41)

Pamene maso anu akuwerenga mawu awa, inu muli nacho chisankho choti mupange: Kodi inu musankha kuti muwakhulupirire Mawu a Mulungu?

Kodi moyo wamuyaya mukakhalira kuti?Zothandizira zake

Yobu 14:12-16

Momwe munthu agona pansi, ndipo osaukanso: kufikira miyamba kulibe, iwo sadzaukanso, kapena kuutsidwa ku tulo take.

O mukadandibisa ine kumanda, mukadandisunga mseri, mpaka wapita mkwiyo wanu, mukadandiikira ine nthawi, ndi kudzandikumbukira ine!

Kodi munthu akafa, adzakhalanso ndi moyo? masiku onse a nthawi yanga yoyikika ine ndidzadikirira, mpaka kudzafike kusandulika kwanga.

Inu mudzaitana, ndipo ndidzakuyankhani: inu mudzakhala nacho chikhumbo pa ntchito ya manja anu.

Pakuti tsopano inu muwerenga moponda mwanga: kodi simuyang’anitsa tchimo langa?

Yobu 19:23-26

O akadalembedwa mawu anga tsopano! o iwo akadasindikizidwa m’bukhu!

Iwo akadazokotedwa pa thanthwe ndi chozokotera chachitsulo ndi kuthira ntovu kwa nthawizonse.

Pakuti ine ndikudziwa kuti muomboli wanga ali ndi moyo, ndipo kuti adzawuka potsiriza pa fumbi:

Ndipo angakhale mphutsi za khungu langa zitaliwononga thupi ili, komabe mu thupi langa ndidzamuwona Mulungu:

Mateyu 7:21-23

Si yense wakunena kwa ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu ufumu wa kumwamba; koma iye wakuchita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba. Ambiri adzati kwa ine tsiku limenelo, Ambuye, Ambuye, sitinanenera mawu mu dzina lanu? ndipo mu dzina lanunso kuturutsa ziwanda? ndipo mu dzina lanunso sitinachita ntchito zambiri zodabwitsa? Ndipo pamenepo ndidzafuulira iwo, ine sindinakudziwani inu nthawizonse: chokani kwa ine, inu akuchita kusayeruzika

Mateyu 22:14

Pakuti oitanidwa ndiwo ambiri, koma osankhidwa ndi owerengeka.

Yohane 3:16-17

Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero kuti iye anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanamtume Mwana wake kwa dziko lapansi kuti akaliweruze dziko lapansi; koma kuti dziko kudzera mwa iye likathe kupulumutsidwa.

Yohane 5:24

Indetu, indetu, ine ndinena kwa inu, Iye amene amva mawu anga, ndi kukhulupirira pa iye amene anandituma ine, ali nawo moyo wosatha, ndipo sadzabwera ku chiweruzo; koma wadutsa kuchokera ku imfa wapita ku moyo.

IAkorinto 2:9

Koma monga kunalembedwa, Diso silinawonepo, ngakhale khutu silinamvepo, ndipo sizinalowepo konse mu mtima wa munthu, zinthu zimene Mulungu wawakonzera iwo amene amamkonda iye.

I Atesalonika 4:13-18

Koma sitifuna kuti mukhale osadziwa, abale, za iwo akugona, kuti mungalire, monganso otsalawo amene alibe chiyembekezo.

Pakuti ngati ife tikhulupirira kuti Yesu anafa nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi iye iwo akugona mwa Yesu.

Pakuti ichi tinena kwa inu mmawu a Ambuye, kuti ife okhala ndi moyo ndi otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye sitidzawatsogolera ogonawo

Pakuti Ambuye mwiniwake adzatsika kuchokera kumwamba ndi mfuu, ndi mawu a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu: ndipo akufa mwa Khristu adzayamba kuuka:

Pamenepo ife okhala ndi moyo otsalafe tidzakwatulidwa nawo pamodzi mmitambo, kukakomana ndi Ambuye mu mlengalenga: ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse.

Chomwecho tonthozanani wina ndi mzake ndi mawu awa.